Jannah Theme License is not validated, Go to the theme options page to validate the license, You need a single license for each domain name.
Chichewa

Akufuna msewu, Admarc ku Tsangano However, the judge found that Chisale’s case did not meet the threshold for certification.

Mfumu yaikulu Mpando ku Ntcheu yalangiza boma kuti liganizire zomanga msika wokhazikika komanso msewu wabwino ku Tsangano m’boma la Ntcheu ponena kuti anthu ake, omwe ambiri amadalira ulimi pa chuma, athandizike. 

Malingana ndi mfumuyo, anthu m’dera lake, monga Amalawi ambiri, ngodzilimbikira pa ntchito zofuna kukweza miyoyo yawo koma amagwa ulesi ndi kusowa kwa zinthu zina zomwe boma limayenera kupereka kwa anthu ake. 

 Mfumuyo imalankhula pa umodzi mwa misonkhano ya kaimaima yomwe mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera, yemwenso akuimira chipani cha MCP pa mpando wa pulezidenti pa chisankho chikudzachi, adachititsa ku Kambironjo m’deralo. 

 Mfundo za Mfumu Mpando zidasokolotsa nthungululu komanso malikhweru kwa anthu omwe adasonkhana, zomwe zidaonetsa kuti mfumuyo idayankhulira ambiri m’deralo.

“Ndimafuna nditsindike pano a pulezidenti, kuti ngati kwathu kuno simutiponyerako msika wa Admarc monga mukunka mulonjezera, komanso kutikonzera mseuwu, anthuwa akhumudwa nanu. 

 “Kuno tinatchuka ndi ulimi, ndipo anthuwa ngoyesetsa. Koma kusowa kwa misika yokhazikika, komwe angamakagule zipangizo za ulimi monga mbewu ndi zina zotero, komanso kukagulitsa zokolola zawo ndi chipsinjo kwambiri pa chitukuko m’dera lathu lino,” idatero mfumuyo. 

 Mfumuyo inadandaula za kuchedwa kukonza kwa msewu wa Ntcheu-Tsangano-Neno-Mwanza. Ntchitoyo yatenga zaka zosachepera 10 chiyambireni, zomwe iyo yati zikusokoneza ntchito zokweza chuma ndi umoyo m’deralo.   

“Ndiyamikire kuti mudatumiza chigiredala chomwe chadzatipalira msewu wathuwu m’masiku apitawo. Komabe ndikadakonda kuti mwina mudakafika chisadatero, kuti mudzamvetsetse kulira kwa anthu anu pa mavuto a mseu mdera lino,” Mfumu Mpando idatero. 

 Msewuwo ndi wa makilomita osachepera 100 posawerengera makilomita ena olumikiza kuchokera pa Tsangano/Doviko kukafika ku maboma a Mwanza komanso Neno. Nthambi ya zomangamanga ya asirikali a nkhondo a dziko lino ya Malawi Defence Force (MDF) ndi yomwe ikugwira ntchitoyo.

Mwa zina, msewuwo omwe ukuchokera pa mphambano ya Tsangano mu msewu wa M1, umalumikiza madera a Sera, Kambironjo, komanso Tsangano mpaka kwa Doviko. Kwa alendo, awa ndi ena mwa madera omwe amatulutsa zokolola za kudimba zochuluka monga mbatata ya kachewere, kabichi, nyemba, ndi anyezi, zomwe madera ambiri a m’tauni, kuphatikizapo Blantyre komanso Lilongwe, amadalira. 

Padakalipano, anthu ambiri, kuphatikizapo alimi eni, amadalira galimoto zikuluzikuku za mtundu wa lorry pa mayendedwe awo, kuphatikizapo kupita ku chipatala.

Nation Online idapeza kuti munthu mmodzi bwezi akupereka mtengo womvererako kukadakhala kuti msewuwo udakonzedwa, Anthu omwe tidayankhula nawo adatiuza kuti pano amakwelera ndalama zosachepera K15 000 mpaka K20 000 mmodzi, kuti mayendedwe atheke chifukwa cha kuvuta kwa nsewuwo, komanso kusakhazikika kwa mafuta a galimoto. 

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button