Chichewa

Anatchereza

Listen to this article

Bwenzi langa akufuna zogonana

Gogo Anatchereza,

Ndine mtsikana wa zaka 19 ndipo ndili pa chibwenzi ndi mnyamata wina.

Koma chomwe chandikhumudwitsa n’choti akundikakamiza kuti tikwatirane ndipo akundiopseza kuti tikapanda kutero chibwenzi chitha.

Gogo ndithandizeni, kodi ndilole kugona naye? Nanga ndikatenga mimba kapena pa matenda?

HHK

HHK,

Usalole kugona ndi mnyamatayo. Ngati akukufuna adikire mpaka mudzakwatirane.

Zaka zako zikuonetsa kuti ukuyenera kukhala pa sukulu. Choncho sukuyenera kupanga zogonana, koma kuika mtima pa maphunziro.

N’zoona ukagona naye zinthu zingapo zitha kuchitika kuphatikizirapo kutenga mimba ndi matenda.

Ndibwino kukhala wopanda chibwenzi kusiyana ndi kumagonana.

Gogo Anatchereza

Kodi mtsikana kufunsira n’kulakwa

Gogo Anatchereza,

Ndine m’modzi mwa atsikana oyimba nyimbo za matamando pa mpingo wina mu mzinda wa Blantyre.

M’gulu lathu muli mnyamata wina yemwe amanditenga mtima kwambiri moti ndimafuna adzakhale bambo wa ana anga mtsogolo muno.

Koma vuto lomwe ndili nalo ndiloti kodi ndingayambitse pati kumuuza za ku mtima kwanga popeza ndine mkazi.

Kodi kufunsira si kwa amuna osati akazi?

Nanga ine nditani, gogo?

GPK

Blantyre

GPK,

N’zoona nthawi zambiri anyamata ndi amene amayambitsa ubwenzi potengera ndi chikhalidwe chathu. Moti mtsikana akafuna kukhala paubwenzi ndi mnyamata zimavuta poyambire.

Koma ine sindionapo vuto mtsikana kumuuza mnyamata za kumtima kwake.

Chikhaledwe chathu chamanga atsikana moti safunsira ngakhale akudziwa kuti uyu atha kukhala mwamuna wabwino womanga naye banja.

Atsikana ambiri amangoonetsero ndi chiyembekezo choti mwamunayo adziwa yekha.

Ndimakhulu lupirira kudzera n’zochita zathu timapereka uthenga wa mphamvu kwa anzathu.

Choncho ndikufuna kukulimbikitsa kuti ngati ukumufunadi mnyamatayu upeze njira yochitira zinthu zomuonetsera chikondi chako.

Related Articles

Back to top button
Translate »