Jannah Theme License is not validated, Go to the theme options page to validate the license, You need a single license for each domain name.
Nkhani

Apempha achinyamata asunge bata

Pamene dziko lino likukonzekera kuponya mavoti Lachiwiri likudzali, wapampando wa bungwe la Machinga District Youth Network a Mphatso Chikaonda apempha achinyamata a m’dziko muno kuti asunge  bata ndi mtendere.

Machinga ndi limodzi mwa maboma omwe kwakhala kukuchitika ziwawa za ndale.

Posachedwapa anthu ena osadziwika bwino adachitira za mtopola mmodzi mwa amayi omwe akufuna kuimira chipani cha Democratic Progressive Party m’chigawo cha ku kummawa kwa bomalo a Ester Jolobala.

Mmbuyomu anthu ena adagenda ndi kuswa galimoto za chipani cholamula cha Malawi Congress Party (MCP).

“Nkhondo siimanga mudzi. Ndale si nkhondo, koma ufulu wosankha atsogoleri. Pa chifukwa ichi, ndikupempha achinyamata anzanga kuti asunge bata ndi mtendere pamene tikuvota Lachiwiri, komanso kudikirira zotsatira za chisankho kuchokera ku bungwe la Malawi Electoral Commission,” atero a Chikaonda.

A Anthony Botha, wapampando wa T/A M’mbelwa Youth Network, akugwirizana ndi a Chikaonda.

Iwo akuti gulu lawo likupanga ndi kutumiza mauthenga m’masamba a mchezo opempha achinyamata a m’bomalo kuti asamachite ziwawa m’misonkhano ya kampeni.

“Tikugwiritsa kwambiri ntchito WhatsApp ndi Facebook kuti uthengawo ufikire achinyamata ambiri,” atero a Botha.

Pamene mlembi wa Rumphi District Youth Network a Jonathan Munthali akuti gulu lawo likuchititsa misonkhano yofotokozera achinyamata kuipa kwa ziwawa za ndale.

“Zinthu zikuyenda ndipo achinyamata ambiri akutimvera,” adatero a Munthali womwenso ndi mtsogoleri wa Rumphi Urban Youth Network.

Mfumu Mizinga ya m’boma la Machinga yapemphanso achinyamata kuti asakopeke ndi ndalama zomwe amalandira kuchokera kwa andale ena kuti azichita ziwawa.

“Mafumu tonse ndife okhumudwa kaamba ka ziwawa zomwe zikuchitika m’boma lino,” iwo atero.

A Mfumu Mizinga akuti mafumu, mabungwe, azipani, komanso apolisi agwirana manja pofuna kuthana ndi zipani m’bomalo.

Mfumu Chikumbu ya m’boma la Mulanje ndi mfumu Mlongoti  ya m’boma la Rumphi apemphanso achinyamata kuti asatengeke ndi ndalama pomachitira ena zamtopola.

Katswiri wa ndale wa ku sukulu ya ukachenjede ya Malawi University of Business and Applied Sciences a Chimwemwe Tsitsi akuti akuluakulu a zipani za ndale ndiwo amakolezera ziwawa.

“Amapereka ndalama kwa achinyamata kuti azichitira anzawo ziwawa. Zipani za ndale ndizo zili ndi yankho pa nkhani yothana ndi ziwawa,” iwo atero.

Maboma ena komwe kwakhala kukuchitika ziwawa za ndale ndi Lilongwe, Blantyre ndi Kasungu.

Mabungwe a Oxfam, National Youth Council, Women Legal Resource Centre, National Initiative for Civic Education Trust ndi ena akhala akupempha achinyamata kuti apewe ziwawa za ndale.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button