Zonga sewero zidachitika pa Kamuzu Stadium pamene Nyerere zidakokera kuuna Shasha pomukayikira kuti ndi wa timu ina yemwe amafuna achite chidima timu yawo. Tikukambamu timuyi yalembera bungwe la Sulom kuti Shasha asamakhalenso pamasewero awo ponena kuti akufuna wovala Shasha azikhala wa timu yawo. Nyerere zikuganiza kuti amene akumavala Shasha ndi wosapotera matimu ena ndipo akufuna…

Akatswiri owona mmene nkhani zandale, chuma ndi zina zikuyendera m’dziko muno komanso anthu wamba ati masiku 100 amene mtsogoleri wa dziko lino Pulezidenti Peter Mutharika wakhala ali pampando wolamulira dziko aonetsa kuti mtsogoleriyu ndi wamasomphenya ngakhale Amalawi ambiri, maka akumidzi, adakalibe munsinga za umphamwi. Ndemangazi zikudza pounguza ulamuliro wa Mutharika m’masiku 100 amene wakwanitsa ali…

Mikangano ya makuponi yabuka

Kulozana zala komanso kuthafulirana Chichewa chamoto zakula m’midzi polembana maina a amene adzalandire zipangizo za ulimi zotsika mtengo. Izi zikuchitika boma litalengeza kuti chiwerengero cha anthu amene alandire zipangizozi chaka chino chikhalabe pompaja pa 1.5 miliyoni monga zidalili chaka chatha. Mafumu, komanso makhansala amene auza Tamvani za nkhaniyi akuti pakhota nyani mchira n’kuchuluka kwa anthu…

Mafumu akuopa Ebola

Mantha a matenda a Ebola agwira anthu okhala m’malire a dziko lino, pamene anthu othawa m’maiko awo akulowabe m’dziko muno ngakhale nthendayi ikupitirira kufala. Izi zapangitsa mafumu a m’mabomawa kupempha Unduna wa Zaumoyo kuti ukhwimitse chitetezo ponena kuti chiyambireni nthendayi undunawu sudafike m’madera awo kuwaphunzitsa za matendawa. Mwachitsanzo, m’sabatayi apolisi m’boma la Karonga kwa Paramount…

Chisankho cha Mulhako chilephereka

Kudali kuthafulirana Chilomwe kusukulu ya pulaimale ya Nyambadwe pulaimale Lolemba masiku apitawa pamene gulu la Mulhako wa Alhomwe ku Ndirande limachititsa chisankho. Chisankhocho chimachitika patadutsa zaka zitatu chisadachitike ndipo amasankha maudindo a mkulu wa gululi ku Ndirandeko komanso wachiwiri wake, mlembi ndi msungichuma. Anthu amene adatsina khutu Tamvani ati chidasokoneza zonse ndi mkulu wina amene amafuna apikisane…

Sabata yatha zidatigwera, Junior Flames kupunthidwa ndi Zambia 2-1. Tisabise, Zambia idasewera bwino. Mwayi ndi goloboyi wathu, apo biii! tidakasamba zenizeni. Ganizo la Ernest Mtawali ndi lakuti akasinthe zinthu ku Zambia. Tingopemphera mwina chozizwa chikachitike koma kuona kwathu izi zikavutirapo. Kukonzekera kwathu nkodandaulitsa. Mpikisano ngati umenewu koma tikungokhala ku Chiwembe pamapeto nkumati takonzeka kukapha Zambia.…

Kusowa kwa magazi, mankhwala ku Qech

Mavuto akhodzokera pachipatala cha Queen Elizabeth Central Hospital (QECH) mumzinda wa Blantyre. Kusowa kwa magazi ndi zipangizo kukuika miyoyo ya odwala pachiswe chifukwa chosowa chithandizo. Lolemba ndi Lachiwiri pamene Tamvani idaswera pachipatalapa m’sabatayi idadzionera zokhoma. Imfa za anthu si nkhani yachilendo, pamene odwala ena angogonekedwa kudikirira tsiku lodzapezeka mankhwala. Dotolo wina amene tidamupeza m’chipatalachi adati vuto lakula…

Chitetezo chalowa nthenya m’malawi

Chitetezo m’dziko muno chaphwasuka. Anthu akuyenda mwamantha pamene ena akuphedwa komanso katundu akubedwa molapitsa. Sabata yangothayi, zigawenga 8 zakhapa mfumu Chisesele ku Madziabango m’boma la Blantyre mpaka kuipha ndi kubanso ndalama ndi mafoni. Nako ku Ntchisi zigawenga zakhapa bambo wina mpaka kupha Lachitatu m’sabatayi. Izitu zikutsatira kuphedwa kwa anthu awiri m’boma la Dedza ndi ena…

Zasolobana kumpando wa chifumu pamene mafumu ena atsopano amene adakwezedwa ndi mtsogoleri wakale Joyce Banda ayamba kuona mbonawona. Tikunenamu, mafumu akuluakulu ena alembera boma kuti lichotse mafumuwa poti adakwezedwa ndi kulongedwa mosatsata ndondomeko yake. Izi zikuchitika pamene mafumu atsopanowa alowa mwezi wachinayi asakulandira mswahara. “Ndalembera unduna wa maboma a ang’ono kuti achotse mafumu amene adakweza…

Mizinda tsopano ili ndi mafumu

Patadutsa zaka 10 dziko lino lisadakhale ndi mafumu a mizinda, iyi tsopano ndi mbiri pamene mafumuwa abwereranso m’mizinda itatu ya dziko lino. M’sabatayi kudali kalikiliki m’mizindayi kusankha mafumuwa. Fumbi lidabonga mumzinda wa Blantyre komwe tsopano kwasankhidwa Noel Chalamanda kuti ndiye mfumu ya mzindawo. Otsatira chipani cha DPP adakwenyana ndi apolisi atamva kuti yemwe amafuna kupikisana…

Zaka 50 zaufulu

Ngakhale mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika akuti dziko la Malawi likuyenera kusangalala pa zomwe lakwanitsa m’zaka 50 za ufulu wodzilamulira, akatswiri ena kudzanso mafumu akuti zifukwa zosangalalira sizikuonekabe poyerekeza kuchuluka kwa zaka. Pamwambo wosangalalira ufuluwu Lamulungu lapitalo, Mutharika adati mwa zina kale dziko lino lidali ndi msewu wa phula wotalika ndi makilomita 96 koma…

‘Chekucheku kuno ayi’

Chigamulo pamwamba pa chigamulo. Patangotha sabata imodzi bwalo lalikulu lamilandu mumzinda wa Blantyre litabwezeretsa T/A Chekucheku wa m’boma la Neno pampando, anthu ena m’bomali ati sakugwirizana ndi chigamulo cha bwalolo kotero achitanso zionetsero zoonetsa mkwiyo wawo. Chekucheku, yemwe dzina lenileni ndi Francis Magombo, adaimitsidwa ndi pulezidenti wopuma Joyce Banda pa 15 May 2014 koma mtsogoleriyo…

Mamulumuzana agwa

Chisankho chapatatu chadza ndi zowawa zake. Pamene mpando wa pulezidenti wakhala wokokerana, mipando ya aphungu nayo yagwetsa mamulumuzana. Omwe ndi akuluakulu pa ndale komanso ena omwe adali nduna mmbuyomu asadabuzika pamipando ya phungu wa Nyumba ya Malamulo. Zotsatira zosatsimikizika ndi bungwe la chisankho la Electoral Commission (MEC) pofika Lachinayi madzulo, zimasonyeza kuti mamulumuzana ena amene…

NGO promotes savings culture in Blantyre

A Blantyre-based non-governmental organisation, A Self-Help Assistance Programme (ASAP), has urged communities to adopt and popularise the culture of saving to put themselves on a sustainable economic footing. ASAP has been running a project to promote community banking and savings in Senior Chief Kapeni in Blantyre which phased out on Thursday. At least 1 075…

Mfundo mbweee kumtsutso

Makandideti 11 amene adasonkhana ku mtsutso wa atsogoleri usiku wa Lachiwiri m’sabatayi alonjeza zodzasintha moyo wa anthu akumudzi ngakhale makandidetiwa akulepherabe kunena zomwe adzachite kuti zomwe alonjezazo zidzachitike. Zikuoneka kuti atsogoleriwo amangonena mawu okoma pokopa anthu. Mwachitsanzo, mtsogoleri aliyense adalonjeza kuti moyo wa anthu akumudzi udzasintha powonetsetsa kuti aliyense wakumudzi ali ndi chochita koma osanena…

Anthu okwiya Lolemba ndi Lachiwiri m’sabatayi adasonkhana paofesi ya DC wa boma la Neno komwe amapempha bwanamkubwayo kuti achotse T/A Chekucheku avulidwe ufumu wandodowu ati chifukwa wanyanya ziphuphu. Mmodzi mwa anthuwa, Steve Donda, wa m’mudzi mwa Donda kwa T/A Chekucheku, akuti mfumuyi ikulanda minda ya anthu, ikumadyetsera ng’ombe zake m’minda mwa anthu komanso ikulonga mafumu…

Mbuzi zadya malo. Patangotha miyezi iwiri mkulu wina ku Nkhotakota atachita chisembwere ndi mbuzi, bambo winanso wamitala ndipo ali ndi ana 9 akuti adatopera pambuzi ku Dedza masiku apitawa. Koma bamboyu, Majaika Salimba, 46, akuti akukhulupirira kuti ‘adalodzedwa’ kuti mpaka umunthu umuchokere posiya akazi ake awiri ndi kukathera chilakolako pambuzi yomwe ati ndi mkota wa…

Zimbalangondo zikhapa achitetezo

Anthu akugona khutu lili kunja, tulo tayamba kusowa, chitetezo chatekeseka ku Soche mumzinda wa Blantyre komwe zimbalangondo zatikita achitetezo a m’deralo la neighborhood watch ndi kuvulaza mmodzi modetsa nkhawa. Izi zachitika usiku wa sabata yathayi Lachiwiri nthawi ili 2 koloko anthu akupha tulo. “Zidalipo zisanu ndi mmodzi (6) ndipo chimodzi chidali ndi mfuti. Zimbalangondozi zidabwera…

Mafumu atekeseka ndi bilu ya malo

Mafumu ena m’dziko muno aopseza kuti achita zionetsero ngati lamulo lokhudza malo lingasinthe kuti iwo asakhalenso ndi mphamvu pogawa malo. Mawu a mafumuwa akudza pamene mabungwe a Landnet, Farmers Union of Malawi (FUM) ndi Women’s Legal Resource Centre (Wolrec) ali yakaliyakali kumva maganizo a anthu pa Bilu yokhudza malo (Customary Land Bill). Pali maganizo oti…

abortion scourge:Hospital registers 51 cases in three months

She is making a killing—literally—through conducting abortions in Mtakataka in Dedza, leaving three girls in serious condition after ‘operations’ went horribly wrong, Nation on Sunday has established. Another girl died in the area following abortion-related complications, according to a chief. It is a costly business that evokes the debate on whether legalising abortion would give…