Chichewa

Chipongwe m’maofesi mwinamu

Listen to this article

Pali maofesi angapo, maka a boma, omwe amachuluka chipongwe kaya titi mwano polankhula ndi anthu ofuna chithandizo.

Ofesi ngati za Immigration, Road Traffic, komanso m’zipatala, kumakhala anthu oti akamakulankhula amachita ngati kuti ndiwe wosazindikira.

Ukafika pakauntala, amakufunsa “tikuthandizeni?” akuyang’ana kumbali kapena ngati akukuyang’ana amakuthira diso loderera kapena lotopa nawe.

Anthu ambiri ogwira ntchito m’malowa amakhala ngati adatopa kalekale. Ukapita kufuna chithandizo ukhoza kuyesa ngati mwayambana. Kulankhula ndi munthu wamkulu ngati akuyankhula ndi mwana.

Nthawi zina kuchipatala akakufotokozera ndondomeko ya kamwedwe ka mankhwala ndiye ukapandakumva bwino umachita kulephera kufunsa kuti afotokozenso kuopa kuzaziridwa.

Ukamafotokoza zowawa m’thupi, usanamalize n’komwe olemba mwankhwala walemba kale. Amachita ngati ukumutayitsa nthawi.

Kukakhala ku Immigration, chipongwe chimayambira ndi mlonda wa pakhomo. Kulankhula ndi anthu mwachipongwe chokweza ngati ukudzapempha pakhomo pake.

Ukalowa mkatimo ndiye mumakhala chidodo cha dzaoneni. Chiimire pamzere mumangomva za mavuto osatha a network.

Ukafika pamalo oti ujambulitse chithuzi kaya chala, anthu ogwira ntchito ambiri amangoyankhula mwamgwazo, moderera ndi mokalipa.

Mabwana kumaofesi ndatchulawa komanso maofesi ena a boma, mutaunika kagwiridwe ka anthu anu antchito, maka awo amakumana ndi anthu, kuti mutithandize izi zichepe.

Phasipoti kaya laisensi ikatha, umachita kuda nkhawa kuti ukapezekenso m’maofesi amenewa.

Kayendedwe ka zinthu m’maofesimu nkotopetsa kale chifukwa, monga ndanena kale, kumakhala chidodo choopsa. n

Related Articles

Back to top button