Nkhani

Chitonzo chakula

Mmodzi mwa akadaulo a momwe ziwalo za m’thupi zimagwirira ntchito, physiology, wati chiwerengero cha abambo amene amakayezetsa ngati ali obereka kapena ayi ndi chochepa zedi.

A Fanuel Lampiao a ku sukulu ya ukachenjede ya KuHeS ati ngakhale abambo amene akhala akukayezetsa ngati ali obereka kapena ayi akuchulukira, abambo ambiri safuna kukayezetsa zomwe zimachititsa kuti azipitirira kukaikira akazi awo kuti ndi osabereka.

“Pa mwezi timayeza abambo 10 kapena 15. Abambo ambiri amaopa chitonzo komanso sadziwa kuti akhoza kuthandizidwa ku chipatala kuti akhale ndi mwana,” adatero iwo.

Malinga ndi a Lampiao, limodzi mwa mavuto aakulu amene amakumana nawo ndi kufooka kwa mphamvu ya abambo ena zimene zimachititsa kuti akanike kuimitsa akazi awo.

“Thandizo la chipatala lilipo pothana ndi mavuto onga awa. Kaamba ka chitonzo, abambo ambiri safuna kubwera kudzayezedwa ku chipatala,” adaonjeza motero.

A Ben Mkangano a zaka 39 adati kukayezetsa ku chipatala kudawathandiza kuti amvetsetse bwino lomwe ndi kuvomereza kuti vuto lidali iwowo.

“Takhala pa banja kwa zaka 8 popanda mwana koma si chitonzo chakecho. Timatchulidwa maina, ati gojo, wakugwa mu mtengo wa papaya ndi zina zambiri. Mbale wina adatilangiza kuti tikayezetse ndipo achipatala atafotokoza kuti vuto ndi ine ndidachivomereza,” adatero iwo.

Iwowa amachokera m’mudzi mwa Semu kwa T/A Chigaru m’boma la Blantyre ndipo adati Amalawi ayenera kuvomereza kuti abambo nawo akhoza kukhala ndi mphamvu zochepera ndipo ichi ndi chifuniro cha Chauta.

Iwo adaonjeza: “Atandipeza kuti ndili ndi vuto, adandipatsa thandizo loyenera. Mmbuyomutu tinkayenda mwa asing’anga kuti asule mkazi wanga. Palibe chimathandiza mpaka pamene adandiyeza ndi kundipatsa thandizo loyenera.”

A Christopher Matchado a zaka 37 omwe ndi mphunzitsi, adati abambo ena safuna kukayezetsa kaamba ka kusadziwa komanso chitonzo chimene chimadza kaamba ka kupezeka ndi vuto la kusabereka.

“Ndine mphunzitsi ndipo chitonzo chachikulu chilipo. Ngakhale kungokalipira mwana kumene makolo ndi aphunzitsi anzanga amandinena kuti ndikuchita zimenezo chifukwa ndine wosabereka. N’zopweteka,” adatero iwo.

Malinga ndi mneneri wa unduna wa za umoyo a Adrian Chikumbe adalimbikitsa abambo amene ali ndi vuto lotere kuti azipita ku chipatala kukalandira thandizo loyenera.

“Kaamba ka kusalana abambo ambiri sapita kukayezetsa kuti athandizidwe. Ambiri mwa iwo safuna adziwike kuti ali ndi vuto lotere,” adatero iwo.

Malinga ndi mmodzi mwa akadaulo a ziwalo za ubereki za abambo a Edem Hiadzi wochokera ku Ghana vutoli limakhudza kwambiri abambo amene ali ndi zaka za pakati pa 20 ndi 45 ndipo mwa mavuto 100 a kusabereka, 20 amakhala okhudza abambo.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Check Also
Close
Back to top button