Jannah Theme License is not validated, Go to the theme options page to validate the license, You need a single license for each domain name.
Nkhani

Lorani mtendere ulamulire

Kampeni ikutha mawa. Atsogoleri atambasula mfundo zawo za chitukuko zomwe zili m’manifesto.

Nawo mabungwe a Oxfam ndi Women Legal Resource Centre (WOLREC) adali pakalikiliki kufotokozera anthu ubwino wovotera amayi, achinyamata ndi anthu aulumali.

Mabungwewa alimbikitsa magulu atatuwa, kuwapatsa luso la ndale, zipangizo zokopera anthu, komanso ndalama zopezera anthu oti awathandize kuyang’anira ndi kuwerengera mavoti awo.

Potsegulira nyengo ya kampeni, a Annabel Mtalimanja, apampando wa Malawi Electoral Commission (MEC), adapempha zipani za ndale ndi otsatira awo kuti achite kampeni yopanda ziwawa.

A Mtalimanja komanso mkulu woona za zipani a Kizito Tenthani adapemphanso atsogoleri kuti kampeni yawo ikhazikike pa mfundo zawo za chitukuko osati kutukwana anzawo ndi kuhonga ovota ndi ndalama.

Ngakhale zipani za ndale ndi atsogoleri awo adasaina mapangano a mtendere, ziwawa zachitika ku Machinga komwe a Ester Solobala, womwe akuimira dera la kummawa kwa bomalo pa mpando wa phungu wa Nyumba ya Malamulo, adachitidwa chipongwe.

Nako ku Kasungu kudali mpungwepungwe. Anthu ena adachita chipongwe otsatira chipani cha Malawi Congress Party (MCP), komanso a Chikondi Kampachike Chisale, womwe akuimira chipanichi m’bomalo.

Ku Mulanje ndi Chikwawa, anthu ena osadziwika bwino adachitiranso anzawo za mtopola.

Zipani za Democratic Progressive Party (DPP) ndi MCP akulozana zala. Wina akuti mnzake ndiye akuyambitsa ziwawa.

Demokalase si nkhondo, koma ufulu wosankha atsogoleri ndi boma la ku mtima kwathu.

Mu ndale za demokalase wopambana amakhala amene ali ndi mavoti ambiri.

Mwa chitsanzo, atsogoleri 17 akupikisana pa mpando wa pulezidenti, koma wopampana akhala mmodzi yekha. Choncho kumvesetsa, kulorerana ndi kuvomereza msanga ndi zinthu zofunika ku demokalase ipite patsogolo.

Pamene tikukwangula kampeni, kuponya mavoti Lachiwiriri likudzali, kudikilira ndi kuulutsa zotsatira za zisankhozi, tiyeni tilole mtendere ulamulire m’mitima, komanso m’madera mwathu.

Ndikufunireni zabwino zonse pamene mukusankha atsogoleri a ku mtima kwanu.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button