Mabungwe akufuna malamulo okhudza AI
Mabungwe a Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR) ndi Malawi Human Rights Commission (MHRC) apempha boma kuti liunikenso malamulo ake pofuna kuteteza nzika zake ku mauthenga a bodza nthawi ya zisankho.
A Michael Kaiyatsa wochokera ku CHRR ndi a Thereza Ndanga a ku MHRC ndiwo adalankhula izi pa zokambirana zomwe bungwe la Paradigm lidakonza posachedwapa.

A Kaiyatsa adati njira za makono zopangira ndi kutumizira mauthenga monga Artificial Intelligence (AI) zadzetsa mavuto atsopano pa nthawi ya zisankho.
“Malamulo athu okhudza kufalitsa mauthenga, sakugwirizana ndi njira za makono zopangira ndi kutumizira mauthenga monga AI,” iwo adatero.
A Kaiyatsa adati Malawi ikufunika kukhazikitsa malamulo ogwirizana ndi momwe njira zopangira, kuunikira ndi kutumizira mauthenga zikusinthira.
Iwo adati anthu ena akugwiritsa ntchito AI kuononga mbiri za anzawo pa nthawi ya chisankho.
Katswiri wa njira za makono zotumizira mauthenga, a Vincent Kumwenda adagwirizana ndi a Kaiyatsa.
“Kusintha malamulo kuthandiza makhoti kuti azigwiritsa mauthenga opangidwa kapena kutumizidwa pogwiritsa ntchito AI ngati umboni,” iwo adatero.
A Ndanga adagwirizana ndi akatswiriwa pa nkhani yoti malamulo azigwirizana ndi nyengo zomwe dziko lino likudutsamo.
“Ngakhale zili choncho, MHRC ikufufuza njira zabwino zotetezera nzika za dziko lino ku mauthenga abodza makamaka nthawi ya zisankho,” iwo adatero.
Ngakhale Malawi Electoral Commission ndi Malawi Police Service akhala akupempha nzika za dziko lino kuti zisamafalitse mauthenga a zisankho abodza, mchitidwe ukupitirirabe.



