Chichewa

Mafuta atsika Lachisanu 

Pamene mafuta ophikira akuyembekezeka kutsika mtengo kuyambira Lachisanu pa 1 April, komishoni yoona kuti pazikhala mpikisano wachilungamo pa malonda la CfTC yati yalandira madandaulo a Amalawi pa zakukwera mtengo kwa mafuta moti akuunikira kuti nkhaniyi itsatidwe mwa ndondomeko kuti Amalawi asafinyike.

Nduna ya zachuma a Sosten Gwengwe, popereka ndondomeko ya zachuma adalengeza kuti boma lachotsa msonkho wa K16.50 pa K100 iliyonse pa mafuta ophikira zimene zapereka chiyembekezo kwa Amalawi kuti kufinyika kwawo kutha. Mafuta akhala akukwera mtengo modabwitsa ndipo akweranso kwambiri kuchokera pomwe a Gwengwe adalengeza zochotsa msonkhowo.

Mkulu wa CfCT a Apoche Itimu adati ntchito yawo si kuyang’ana za mitengo koma kuonetsetsa kuti ogula sakudyeredwe masuku pamutu.

“Tamva kale nkhawa za anthu zokhudza mitengo ya mafuta ophikira kaamba ka kuchotsedwa kwa VAT ndipo tikuunikira bwinobwino. Tamva kale nkhawa zimenezo ndipo tikuunika kuti zikhala bwanji koma cholinga chathu n’choti Amalawi asaponderezedwe pa nkhani ya mitengo,” adatero iwo.

Nkhawa za Amalawi zachoka poti nduna ya zachuma italengeza zochotsa VAT pamafuta ophikira, makampani adakwenzanso mitengo ndipo chokayikitsa n’choti mwina potsitsa chifukwa cha VAT mitengoyo ikhoza kungobwerera pomwe Amalawi ankadandaula n’kale VAT ilipo.

Malingana ndi kalata yochokera kuunduna wa za malonda, makampaniwo adavomera kuti atsitsa mtengo wa mafuta potsatira kuchotsedwa kwa msonkhowo.

“Tikulengeza kuti kutsatira mkumano wathu ndi makampani owenga mafuta ophikira, iwo adavomera kuti atsitsa mitengo yawo ndipo kampani iliyonse idzadziwitsa undunawo za mitengo yake,” yatero kalatayo yomwe adasaina ndi mlembi wa undunawo a Christina Zakeyu.

Ndipo pomwe makampani sadawinyewinye pa zotsitsa mafutawo poti ndi lamulo la boma, akadaulo enanso ati Amalawi asayembekezere kusintha pa kulimba kwa moyo.

Koma mkulu wa bungwe loimira anthu ogula la Consumers Association of Malawi (Cama) a John Kapito ati mtengo wa mafuta ophikira sikununkha kanthu pa zifukwa zomwe zikulimbitsa miyoyo ya Amalawi.

“Mtengo wa mafuta ukukhudzana bwanji ndi kugwa kwa mphamvu ya Kwacha? Pali zinthu zoyenera kutsitsa mitengo kupambana mafutawo monga madzi, chimanga koma palibe akukamba za zimenezi ngakhale kuti msonkho wa madzi nawo udachotsedwa,” atero a Kapito.

Iwo ati kulimba kwa moyo wa Amalawi kungathe pokhapokha patapezeka ndondomeko zothandiza kusunga mphamvu ya Kwacha komanso kuunika bwinobwino mitengo ya zinthu zofunikira kwambiri pamoyo wa munthu.

A Bernard Mphepo woyendetsa mapulogalamu a zachuma ku bungwe la Centre for Social Concern (CfSC) ati masiku ano moyo unadula kwambiri kotero mpofunika kukonza zambiri kuti anthu apeze mpata opumira.

“Padakalipano, banja la anthu 6 limafunika K210 000 mwezi onse ndiye chofunika n’kupeza njira zoti kodi anthuwo angakwanitse bwanji kupeza ndalamayi,” atero a Mphepo.

Iwo ati boma likuyenera kuunika mitengo ya zinthu zosiyanasiyana zakudya komanso zomwe sizakudya koma n’zofunika pamoyo wa munthu tsiku ndi tsiku.

“Boma likuyenera kulingalira za mitengo yokhazikika ya chimanga, mbeu zakudimba ndi kumunda, nsomba, nyama, sopo, mchere, shuga ndi zinthu zina zofunika pamoyo wa munthu. Pamenepo mpomwe tingalimbe mtima kuti moyo ufewa,” adatero a Mphepo.

Iwo adaonjeza kuti pamapulani ake, boma litsogoze ntchito za mafakitale kuti katundu wambiri azipangidwa m’Malawi momwe muno kuti azikhala otsika mtengo komanso lichilimike ntchito zaulimi kuti zipangizo zopangira katundu m’mafakitale zizipezeka.

A Grace Samson Banda a kwa Ngwangwa ku Lilongwe ati nkhani yotsitsa mtengo wa mafuta ndi yolandiridwa koma adati mpofunika kudikira mpakana mafutawo atatsitsidwa mtengo kusiyana n’kubwekera msanga.

“Paja nthawi zina za ku Malawi zimatha kusintha poyerayera ndiye tidikire kaye adzalengeze kuti atsitsa osati kungoti akambirana zotsitsa mtengo basi tayamba kale kuomba m’manja ayi,” adatero a Banda.

Malingana ndi kalata ya mgwirizano pakati pa unduna wa zamalonda ndi makampani owenga mafuta, undunawo uzionetsetsa kuti mbewu zopangira mafuta monga soya sizikutuluka mwachisawawa m’dziko muno kuti makampani asamasowe zipangizo.

Koma undunawo wachenjezanso kuti ukaona kuti makampaniwo sakutsitsa mtengo wamafutawo, iwo udzakhwefula kuti mafuta akunja akhoza kulowa mwakathithi kuti polimbirana msika, mitengo idzatsike.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button