Chichewa

Mphwiyo, Kasambara akadali m’chitokosi

Listen to this article

 

 

Pamene bwalo la milandu ku Lilongwe likupitiriza kumva nkhani za amene akuwaganizira kuti adatengapo gawo posolola ndalama za boma, yemwe adali woyendetsa chuma cha boma Paul Mphwiyo komanso nduna yakale ya zachilungamo Ralph Kasambara akadali m’chitokosi.

Akadali mkati: Mphwiyo

Kasambara akuyankha mlandu womuganizira kuti adakonza chiwembu chofuna kupha Mphwiyo pamene Mphwiyo akuyankha mlandu womuganizira kuti adatengapo gawo poba K2.4 biliyoni ya boma. Iye adamangidwa Loweruka lapitalo pomwe oganiziridwa ena pamlanduwo Auzius Kazombo Mwale, Clemence Mmadzi ndi Roosevelt Ndovi adatulutsidwa pabelo Lachitatu.

Lachinayi, wachiwiri kwa mkulu wa bungwe lothana ndi ziphuphu la Anti-corruption Bureau (ACB) Reyneck Matemba yemwe amaimira boma pamlanduwo mmalo mwa mkulu wa oimira boma pamilandu Mary Kachale adapempha wogamula Esmie Chombo kuti Mphwiyo asungidwebe m’chitokosi kwa sabata ziwiri.

“Apolisi ofufuza za ndalama apeza maumboni ena okhudzana ndi Mphwiyo ndipo potha sabata ziwiri akhala atamaliza zofufuza zawo. Ngati adzakhale asanamalize, tidzalola kuti atuluke. Sikuti tikungofuna kumuzunza,” adatero Matemba.

Mphwiyo ali ndi milandu 17 yokhudza zosololazo.

Ndipo woweluza kubwalo lalikulu la Lilongwe Rezine Mzikamanda dzana adati pofika Lachisanu sabata ya mawa, Kasambara adzakhala atadziwa ngati angatuluke kapena ayi. Izi adanena woimira Kasambara Modecai Msiska adapempha bwalolo kuti litulutse Kasambara chifukwa woweluza Michael Mtambo adabweretsa nkhani yoti Kasambara asakhalenso pabelo kukhoti yekha nkulamula kuti Kasambarayo alowenso m’chitokosi.

Kuomberedwa kwa Mphwiyo pa 13 September 2013 kudavumbulutsa kusolola kwa chuma kumene kunkachitika m’boma. Kasambara akuzengedwa mlandu wokonza chiwembu chopha Mphwiyo limodzi ndi MacDonald Kumwembe ndi Pika Manondo. n

Related Articles

Back to top button