Chichewa

Ndinkacheza ndi mchimwene wake

Listen to this article

 

Akuti amapitapita kunyumba kwa namwali potengera chinzake chomwe chidalipo pakati pa iye ndi mchimwene wa namwaliyo.

Adagwiriziza kale unkhoswe: Emmanuel ndi Hawa
Adagwiriziza kale unkhoswe: Emmanuel ndi Hawa

Emmanuel Katiko akuti nthawi zonse amasowa tulo kulingalira za Hawa Mulele koma amalephera kumasuka powopa kuononga chinzake.

“Tinkakhala limodzi ku Chiwembe mumzinda wa Blantyre ndipo mchimwene wake adali mnzanga koma ine  maso adali pa mchemwali wakeyo” adatero Emmanuel.

Iye adati m’chaka cha 2009 ndipo adalimba mtima nkufunsira msungwanayo ndipo zidatheka mpaka madongosolo kuyambika.

Pa 7 November 2011 chinkhoswe chidachitika ku Chiwembe komweko ndipo akuti akuyembekezera ukwati woyera.

Iye adati adasangalatsidwa ndi Hawa chifukwa cha khalidwe lake lofatsa ndi lodzichepetsa komanso kudzilemekeza.

Hawa adati kwa iye kukwatiwa ndi Emmanuel ndi chinthu chapamwamba chomwe amalakalaka chitamuchitikira.

“Zidayenda momwe ndinkafunira. Timakondana ndiposo ndi mwamuna wabwino woopa mulungu ndi wachikondi,” adatero Hawa.

Awiriwa akuti akufuna Mulungu awatsogolere muulendo wawo wa banja kuti adzakhale limodzi mpaka kale popanda chosokoneza.

Emmanuel amawochokera kwa T/A  Malemia ku Zomba pomwe Hawa kwawo ndi kwa T/A Mpama ku Chiradzulu. n

Related Articles

Back to top button
Translate »