Chichewa

Ngozi za kabaza zanyanya 

Listen to this article

Boma ladandaula kuti ndalama zochuluka za bajeti ya zaumoyo zikulowa pothandiza mavuto opeweka monga ngozi zapamsewu zokhudza akabaza a njinga zamoto.

Malingana ndi lipoti lomwe unduna wa zamtengatenga ndi mtokoma udatulutsa sabata yatha, ngozi za kabaza wa njinga zamoto zidakwera kuchoka pa 71 mu 2014 kufika pa 2 268 mu 2021.

Izi zikutanthauza kuti anthu omwe adathandizidwa m’zipatala kaamba ka ngozi za kabaza wanjinga zamoto adaonjezekera ndi 90 mu 2021 kuchoka pa munthu mmodzi yemwe amathandizidwa mu 2014.

Ndipo Lolemba pomwe amayendera nthambi ya zamafupa pachipatala cha Kamuzu Central Hospital, mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera adazizwa kuti anthu 8 mwa 10 amene adali muwodiyo adavulala pangozi za kabaza.

A kabaza amapakira mopyola muyeso

“Izi n’zachisoni. Tiyenera kukonza njira kuti ngozi za kabaza zichepe m’dziko muno. Momwe tinkanena kuti pakhale ndondomeko za kabaza, ena ankayesa ndi ndale koma onani lero,” adatero iwo.

Polankhula ndi Tamvani, wachiwiri kwa nduna ya zamtengatenga ndi mtokoma a Nancy Mdooko adati chipsinjochi chakulira kwambiri zipatala zikuluzikulu chifukwa zipatala zing’onozing’ono zimatumiza matenda oterewa m’zipatalazo.

“Tangoganizani kuti m’chaka cha 2021 chokha, chipatala cha Kamuzu Central chidalandira anthu angozi za kabaza wanjinga zamoto okwana 2 122 nanga m’zipatala zinazo zidali bwanji,” adatero a Mdooko.

Iwo adati mwa anthu angozi zakabaza wanjinga zamotowo, anthu 144 adamwalira mchaka cha 2021 kuyerekeza ndi anthu 28 omwe adamwalira m’chaka cha 2015.

Lipoti la undunawo likuti ngozi zambiri zamtunduwu zimachitika kaamba kakusatsata malamulo apamsewu makamaka amomwe wanjinga amayenera kuyendera pamsewu komanso kunyamula katundu ndi anthu mpyola muyeso.

“Titaunika chomwe chikuchititsa izi, tidapeza kuti akabaza ambiri alibe ziphaso zoyendetsera njinga komanso sadapange maphunziro alionse oyendera pamsewu choncho amangoyendapo mulimonse.

“Chifukwa china nchoti ambiri sasamala za kapakilidwe chifukwa njinga imodzi imatha kunyamula anthu anayi opandanso zodzitetezera kapenanso kuphatikiza anthu ndi katundu wambiri,” latero lipotilo.

Phungu wa Dowa Ngala a Arthur Sungitsa adati lipoti la undunawo likunena zoona chifukwa akabaza a njinga zamoto satsata mbali yoyenera podutsa galimoto kapena ogwiritsa ntchito msewu ena.

“Nthawi zina umangodzidzimuka kuti njinga yakudutsa kumanzere, ukati utere ina iyo yadutsanso kumanja ndiye munthu utati ukufuna kukhota mwadzidzidzi sungawaphe anthu amenewa?” adatero a Sungitsa.

Iwo adati mwina zingathandize nthambi yoona zapamsewu itatsegula nthambi zake m’maboma akabazawo asamavutike akafuna kutenga ziphaso zoyendetsera njingazo chifukwa mwina ena amagwa ulesi ndi mtunda.

Kabaza wa njinga zamoto adatentha kuchoka m’chaka cha 2013 boma lomwe lidalipo nthawiyo la People’s Party litachotsa msonkho pa njinga zamotozo ndi kupatsa mpata achinyamata kuyendetsa kabaza momasuka.

Nzika ina ya mumzinda wa Blantyre a Jordan Chigwenembe adadzudzula  apolisi kaamba kolekerera a kabaza kumangoyenda opanda zoyenera komanso kunyamula mopyola muyeso. Iye adachenjeza anthu kuti ayenera kusamala ndi a kabaza ena chifukwa pambali pangozi, enanso ngakuba komanso achipongwe.

“Makolo ambiri masiku ano amalekera ana awo ndi a kabaza kuti azikasiya ndi kutenga anawo kusukulu. Aonetsetse kuti mwana wawo akuyenera kukhalapo yekha panjingayo. Makolo tizionetsetsa kuti njinga ili bwino ili ndi kalilole komanso woyendetsa asakhale wopsontha delunde ndi zina,” adatero iwo.

Iwo adati n’kofunika kusamala makamakanso anawo akakhala aakazi chifukwa nkhani za a kabaza kugwirira ana zakhala zikumveka.

“Ndi bwino pambali pokhala ndi nambala ya akabazawo, tizisunganso nambala ya mkazi wake ndi anzake awiri kuchitira pamawa,” adatero iwo.

A Ganizani Msukwa a ku Lilongwe ati zimangovuta kuti palibe malamulo enieni ounikira ntchito za kabaza koma ntchitozo n’zothandiza chifukwa achinyamata ambiri akupezapo chochita komanso kabazayo amafupikitsa ulendo.

“Boma likadangopanga malamulo ounikira momwe akabaza angapangire bizinesi yawo chifukwa kunena zoona, kabaza akuthandiza mabanja ambiri pa zachuma komanso anthu ofuna kuyenda msanga amadalira kabaza yemweyo,” adatero a Msukwa.

Nduna yazachitetezo cha m’dziko a Jean Sendeza adati unduna wawo kudzera ku nthambi ya zapamsewu umagwira ntchito ndi mabungwe a akabaza powaphunzitsa zokhudza pamsewu komanso malamulo.

“Nthambi yathu yoona za pamsewu idayamba kale kukumana ndi akabaza anjinga zamoto kuwaphunzitsa kuti malamulo apamsewu akuti bwanji nanga oyenda panjinga akuyenera kuyenda bwanji.

“Kupatula apo, timawalimbikitsanso kuti azikachita maphunziro oyendetsera njinga nkutenga ziphaso komanso azikhomera njinga zawo kuti tizitha kulondoloza pakachitika ngozi,” adatero a Sendeza.

Related Articles

Back to top button