Phindu la kusankhiratu fodya pothyola
Mlimi akasankhiratu fodya wake pamene akuthyola, kusoka ndi kuumitsa, amapeza phindu lochuluka kusiyana ndi kumangomusakaniza ndi kudzasankha atamuumitsa kale.
Alangizi akuti izi zili chomwecho chifukwa zimathandiza kuti mlimi aike fodya wofanana m’belo limodzi ndipo sasemphanitsa.
Zotsatira zake, mlangizi wa mbewuyi ku bungwe la Agriculture Ressearch and Extension Trust (Aret) Maurice Mantchombe adati mlimi amagulitsa pa mtengo woyenera komanso amapulumutsa ndalama zimene amayenera kuononga akamubweza kuti akayambirenso kusankha.
“Kusankhiratu kumathandiza kuti fodya akhale wofanana mtundu, kutalika ngakhale michere yake chifukwa sasakanikirana.
“Zotsatira zake, amakhala pamlingo umene ogula amafuna choncho mlimi amapeza phindu lochuluka,” iye adatero.
Mantchombe adaonjeza kuti fodya wotereyu savuta kuumitsa chifukwa cha kufananaku.
Iye adati chifukwa choti amamupatula, chisamaliro chimakhala chabwino choncho sapezeka ndi zinyalala.
Mlangiziyu adati mlimi amadzichepetsera ntchito ndi nthawi chifukwa akauma, savutika ndi kusankha.
Iye adati njirayi imathandizira kuti fodya wapansi yemwe amakhala ndi dothi, asaipitse wapakati kapena wapamwamba.
“Ogula amadziwa kuti fodya wapansi amakhala wa matope choncho akakhala m’belo lake, mlimi amagulitsa molingana ndi mtengo wa fodya wa geledi imeneyo pa msika.
“Mlimi akasoka kapena kuumitsa pamodzi fodya wotereyo ndi wabwino, yense amaipa ngakhale atamusankha choncho amamugulitsa pa mtengo wotsika ngati omwe akadagulitsira wa pansi,” adafotokoza motero.
Mlimi wina wa fodya wa m’boma la Kasungu David Nekhantani adati kusankhiratu fodya pomwe akuthyola kumamuthandiza kugulitsa mwachangu komanso pa mtengo wabwino.
Iye adati mitengo ya fodya kumsika imasinthasintha makamaka nyengo yogulira ikamapita kumapeto choncho amamaliza mwachangu chifukwa sataya nthawi ndi kumasankha atauma kale.
“Kusankha fodya woti wauma kale ndi ntchito yofuna nthawi yaitali chifukwa kumalira kuti ugwire tsamba lililonse. Izi zimapangitsa kuti mlimi amalize mochedwa mapeto ake, amakapeza misika itapenga,” iye adatero.
Lackson Chikwapulo yemwe amachitanso ulimi wa mbewuyi m’boma la Chirazulu adati kupatula kupindula adazindikira kuti njirayi ndi yophweka kusiyana ndi kusankha atauma kale.
Iye adati amangoonetsetsa kuti pa tsiku azithyola masamba awiri oyang’anizana pa mtengo uliwonse wa m’mundamo.
Akachoka apa, mlimiyu adati amamusoka, kumuyanika, kumusunga, kumumanga ndindi ndi kumudindira pamodzi.
“Timachita izi pa masamba awiri alionse a fodya omwe takhala tikuthyola m’mundamo osawasakaniza,” iye adatero.
Mantchombe adakumbutsa alimi kuti akuyenera kusamala ndi zinthu monga ulusi wa masaka, mapepala ndi nthenga za nkhuku pamene akuthyola ndi kuumitsa chifukwa zimamata ku fodya.
Popewa izi, iye adati mlimi asanyamulire fodya wake m’thumba la saka kapena pepala pamene akuchoka naye kumunda.
Mlangiziyu adati zoterezi zimavuta kuziona ngakhale mlimi asankhe choncho zimakaonekera kumsika.
“Fodya akakhala wamuwisi, amakhala ndi mafuta omwe amachititsa zinthu monga ulusi wa matumba, mapepala ndi nthenga za nkhuku, zizimatirira mosavuta,” iye adatero.
Chifukwa cha ichi, iye adati ndi bwino kuti alimi azigwiritsa ntchito zinthu monga madengu, ngolo ndi zina zomwe sizingamatirire ku fodya.
Kuonjezera apa, mlangiziyu adati mlimi akuyenera kutetezera m’chigafa momwe akuyanika fodya wake ku zinthu monga nthenga za nkhuku pamene akuyanika fodya.