Chichewa

Thirani feteleza nthawi Yabwino, moyenera

Listen to this article

Mlimi akhoza kukonza m’munda moyenera, kubzala mbewu yabwino ndi moyambirira komanso kuthana ndi tchire koma osapeza zokolola zoyenera akaphonya pankhani ya feteleza.

Malingana ndi oona za feteleza ku nthambi ya zakafukufuku wa zaulimi ya Bvumbwe m’boma la Thyolo, mlimi ali ndi kuthekera kopeza zokolola zochuluka ndi magawo 90 pa magawo 100 alionse akathira feteleza m’nthawi ndi mlingo woyenera komanso akatsatira ndondomeko.

Iye adafotokoza kuti nthawi yoyenera kuthira feteleza wokulitsa ndi pobzala kapena chikangomera kumene pasadapite masiku 7.

“Feteleza wobereketsa timalimbikitsa kuti mlimi athire pakatha masiku 21 kuchokera pamene wathira wokulitsa choncho akasemphana ndi nthawi imeneyi amachisokoneza ndipo sichichita bwino,” iye adatero.

Mfune adati ntchito ya feteleza wokulitsa ndiyochititsa chimanga kuti chikule choncho akuyenera kuthiridwa chisadayambe kukula kuti achikulitse mwamphamvu.

Kuthira feteleza uku n’kolakwika chifukwa mlingo sakuudziwa bwino

Iye adaonjeza kuti chimanga chikakula mwamphamvu ndi kukumana ndi feteleza wobereketsa nthawi yabwino chisadafike popanga chiganizo chobereka chimachita bwino kwambiri.

Mfune adafotokoza kuti mlimi akathira feteleza chimanga chitapanga kale chiganizo sagwira ntchito bwino.

“Mbewu zathu ndi chinthu chamoyo ndithu ndipo cholinga chake chimakhala choti chikule ndi kubereka.

“Chiganizochi mumbewu chimachitika m’sabata ziwiri zoyambirira mlimi akangobzala ndipo mlimi akathira feteleza wokulitsa mopyola masiku tanenawa imakhala itachepetsa kale kukula.

“Izi zili chomwechi chifukwa chiganizo chimakhala chasintha ndipo chikubwera ndi chobereketsa,” iye adatero.

Mfune adati mlimi akathira wobereketsa chitapanga kale chiganizo sichibereka bwino chifukwa mphamvu zimakhala zochepa choncho alimi akuyenera kuonetsetsa kuti azithira feteleza ziganizo zisadachite mu mbewu kuti apewe izi.

Iye adadzudzula mchitidwe wosakaniza feteleza ponena kuti izi zimachititsa kuti mlimi athire feteleza mochedwa komanso mlingo wake sukhala woyenera.

Mlangizi wa mbewu m’boma la Dedza Madalitso Machira adathirirapo ndemanga kuti kuthira feteleza wochepa kumachititsanso kuti chimanga chisabereke moyenera.

“Alimi ena amathira ochepa akathira manyowa koma sakuyenera kutero pokhapokha ngati amatsatira ndondomeko popanga manyowawa komanso akuthira moyenera ndipo pamapeto pake atsimikizika kuti chonde chabwerera m’munda mwawo.

Mphunzitsi wa zaulangizi ku Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar) Paul Fatch adaonjeza kuti manyowa amathandiza kugwira feteleza kuti asapite pansi asadagwire ntchito yake.

Iye adafotokoza kuti izi zimathandiza kuti mbewu ikhale ndi nthawi yotenga feteleza ndi kugwiritsa ntchito bwino.

“Kukachita ng’amba ndiye kuti chinyotho chimasungika kwa nthawi yotalikirapo m’nthaka muja choncho feteleza amagwiritsa ntchito chinyonthocho kuti apindulire mbewu,” iye adatero.

Malingana ndi buku la “Practical Guide to Maize Production in Malawi’ limene adasindikiza ndi akatswiri a zaulimi a kunthambi ya zaulangizi Department of Agriculture Research Services (Dars), limodzi mwa mavuto aakulu amene ulimi wa chimanga ukukumana nawo m’dziko muno ndi kuchepa kwa chonde m’nthaka.

Kuchepa kwa chonde m’nthaka ndi chinthu chimene chikuchititsa kuti makono ano alimi azipeza zokolola zochepa kusiyana ndi kale.

Bukuli lidatsindika kuti ichi ndi chifukwa chake alimi akuyenera kuthira feteleza ku chimanga nthawi yabwino, moyenera ndi pamlingonso woyenera kuti azipeza zokolola zochuluka.

Werengani patsamba lachitatu kuti mudziwe kuchuluka kwa feteleza amene mukuyenera kuthira m’munda mwanu, kathiridwe koyenera ndi zinthu zimene mukuyenera kupewa kuti agwire bwino ntchito.

Related Articles

Back to top button
Translate »