Chichewa

Ulemu kwa Geoffrey Mwale

Listen to this article

Mkuluyo adali msilikali. Aliyense pa Wenela amamudziwa bwino. Akangoti waledzera, tsikulo ndiye kumakhala ndewu zafumbi. Akapanda kupeza womenyana naye pa Wenela, zonse zimakathera kwa mkazi wake.

Tonse tikudziwa kuti samasiya ndalama za ndiwo pakhomo msirikaliyo. Mkazi amati akafunsa ndalama ya pakhomo, makofi. Akati anawa chakudya, kukunthidwa ngakhale ndi zitsulo.

 

“Ukhoza kukachita ngakhale uhule upeze yodyetsa anawa,” adali kutero msirikaliyo.

Koma akangomva kuti mwamuna wina kumsika wamupatsa mkaziyo bonya waulere, nayenso ali pamoto.

Adali wozunguza.

Ngakhale kupita kutchalitchi adaleka kalekale. Ena ankamutcha Boko, ena akuti Isisi. Koma adali msirikali basi.

Tsiku lina adautunga kuyambira mmawa mpaka usiku. Amachoka kumowako nthawi itangodutsa 10 koloko. Wapamalopo atafunsa kuti amulipire, adalandira zibakera.

Atafika kunyumba, adapeza kalata ili pakhonde.

Chigawenga msirikali woipitsa dzina la asirikali anzako, munthu wa nkhanza kuposa Satana. Wandizunza mokwanira, ndamanga ulendo wakwathu. Komabe ndakusiyira chakudya chimene anzako anagula. Ndatengedwa ndi anzakowo, munthu wopanda nzeru iwe. Kukhakhala mtima ngati wakwananda kapena msana wa fulu. Estere.

Estere adali mkazi wa msirikaliyo. Adalowa m’nyumba. Adafikira patebulo pomwe padali mbale ziwiri zovindikira. Adadziwiratu kuti mwinamo mudali nsima, mwinamo ndiwo. Kukhosi kudachita kuti dyokodyoko. Dovu lidati liyambe kuchucha.

Adayamba wasamba m’manja. Nthawi yopemphera adalibe. Mtima udali kugunda. Adavundukula mbale yoyamba, mudali miyala itatu. Miyala, osati mitanda itatu!

Adatsegula mbale yachiwiri. Mudali masamba awiri a gwafa osaphika nkomwe. Adali atathiridwa tomato ndi mchere.

Msirikali adakwiya. Adayatsa fodya wamkulu amene ankasunga mujombo. Adayamba kukoka. Utsi sumatuluka nkomwe, amaupanirira. Amachita ngati akubanika.

Atatha kusutako, adakhala pansi. Momwe adagonera sadadziwe! Adayamba kulota.

Adalota kuti adali atamwalira. Adafika kumwamba, pampando wachifumu. Woweruza anthu abwino ndi oipa adamuuza mkuluyo kuti adamupatsa mwayi wolapa koma iye sadafune kulapa. Adamupulumutsa kungozi komanso matenda koma sadafune kulapa. “Udali kukonda ndewu, kumenya mkazi ndi ana ako. Tsono ndikupatsa mwayi umodzi wobwerera kudziko lapansi. Subwerera ngati munthu. Sankha chinyama chimene ukufuna,” adatero woweruzayo.

Msirikali uja adayamba kudya mutu: “Ndisanduke mkango? Ndikaphaphalitsa nyama zina zakutchire. Koma ayi, alenje akandipha chifukwa akufuna chikopa, mchira ndi matumbo anga. Ndisanduke njovu, nyama ndi anthu azikandiopa. Koma ayinso, mnyanga wanga ukandiphetsa! Nanjinanji kusanduka nyani ndiye sindikalimba. Akandipha kuopa kuwapatsira ebola.”

Pamapeto pake, adasankha kukhala kangaude. Choncho nditsetsereka kudziko nkukakhala m’nyumba yogumuka zakazaka. Womulenga adamuuza: “Chabwino, usanduka kangaude. Bwerera kudziko lapansi.”

Apa mpomwe mkulu uja adadziwa kuti tsopano azitulutsa ulusi muja achitira kangaude. “Hmmmmm! Hmmmmm!” adali kutero, uku akumva kuti ulusi ukutuluka ndipo iye akutsikira kudziko lapansi.

“Hmmmm! Hmmmmm!” adapitiriza, ulusi ukutuluka. Posakhalitsa adayamba kuona dziko lapansi.

“Hmmmm! Hmmmmm!” adatsikirabe, ulusi ukutuluka. Kenako adafika padziko lapansi.

Adayang’ana kumwamba ndipo dzuwa lidamuthobwa m’maso. Apa mpamene msirikaliyo adadzidzimuka kutulo kwakeko. Poti atembenuke, adazindikira kuti wadzionongera.

Abale anzanga, mwinatu sindidakuuzeni, msirikaliyo ndi mmodzi mwa asirikali amene adamenya mnyamata wina timu yawo itagonja pampira wa dolola umene udalipo pa Wenela. Mnyamatayo adatisiya momvetsa chisoni, ndipo pano msirikaliyo limodzi ndi anzakewo sakudziwika kumene ali.

Tonse pa Wenela takhudzidwa ndi imfa ya Geoffrey Mwale! Chiyembekezo chathu nchakuti Moya Pete alowererapo pankhaniyi ndipo msirikali wa maloto limodzi ndi anzake achiwembuwo agwidwa! Si zoseka!

Gwira bango, upita ndi madzi!

 

 

 

Related Articles

Back to top button