Chichewa

Wofuna kuba alubino amusinthira mlandu

Listen to this article

Mkulu yemwe akuimbidwa mlandu wofuna kuba alubino ndi cholinga chomupha zidamuthina Lachiwiri lapitali kubwalo la milandu la majisitireti ku Mzuzu pomwe boma lamusinthira mlandu.

Tsopano Phillip Ngulube, wa zaka 21, akuyankha mlandu wofuna kupha munthu, womwe ndi waukulu kuposa wozembetsa munthu ndi cholinga chofuna kumupha.

Wa kulimandi: Ngulube (kumanzere) pambuyo pokaonekera kukhotiWa kulimandi: Ngulube (kumanzere) pambuyo pokaonekera kukhoti
Wa kulimandi: Ngulube (kumanzere) pambuyo pokaonekera kukhotiWa kulimandi: Ngulube (kumanzere) pambuyo pokaonekera kukhoti

Ngati Ngulube angapezeke wolakwa pamlandu watsopanowu akhoza kukakhala kundende moyo wake wonse.

Ngakhale Ngulube adavomera mlandu woyambawu pa September 15 pomwe adakaonekera kubwaloli koyamba, mlandu watsopanowu waukana.

“Ndikukana kuti ndinkafuna kumupha mtsikanayu. Zoona zake ndi zoti ndinkamufuna banja basi,” iye adauza bwaloli.

Yankholi lidadzi-dzimutsa majisitireti Gladys Gondwe chifukwa woganiziridwayu ankangoyenera kunena ngati akuuvomera kapena kuukana mlanduwu.

Komabe woweruzayu adalemba kuti waukana poti woimira boma pamlanduwu ayenera kupereka umboni mwatsatanetsatane kuti cholinga cha woyankha mlanduwu chidali kupha chibwezi chakecho.

Wapolisi woimira boma pamlanduwu, Christopher Katani, adalonjeza kuti abweretsa mboni zisanu ndi ziwiri pamene bwaloli lidzakumanenso pa September 30. Zina mwa mbonizi ndi Mswahili yemwe akuti adatsatsidwa malonda a mwalubinoyo kuphatikizapo mtsikana mwini wakeyo.

Malinga ndi mneneri wa apolisi m’chigawo cha kumpoto, Maurice Chapola, oimira boma pamlanduwu aganiza zosintha poyesayesa kuti ozunza maalubino azilandira zilango zokhwima pofuna kuthetsa mchitidwewu.

Bwalo la milanduli lidamva kuti Ngulube, yemwe amagwira ntchito ya uphunzitsi modzipereka pasukulu ya pulaimale ya Mongo, adafunsira mbeta mtsikana wachialubino, wa zaka 17, ndi cholinga chofuna kumuba kuti akamugulitse pamtengo wa K6 miliyoni.

Kupha ndi kugulitsa anthu achialubino, makamaka ana, wayamba kukula m’dziko muno pamene boma la Tanzania laletsa using’anga m’dzikomo womwe akuti wapangitsa kuti maalubino ambiri aphedwe ndi anthu ofuna zizimba.

Ku Tanzania ndi maiko ena a kuvuma kwa Africa ena amakhulupirira kuti ziwalo za munthu wachialubino ndi zizimba zopangira mankhwala ochulukitsira chuma ndi mwayi.

Related Articles

Back to top button
Translate »