Chichewa

Women yakhazikitsa manifesito

Akatswiri omenyera ufulu wa amayi akuti manifesito ya amayi ndi chida cha mphamvu chosinthira moyo wawo pa ndale m’dziko muno.

Akatswiriwa adalankhula izi pa mwambo wokhazikitsa manifesito ya amayi womwe udakonzedwa ndi Women’s Manifesto Movement (WOMEN) ku Lilongwe.

Polankhula pamwambowo, katswiri womenyera ufulu wa amayi wa m’dziko la South Africa a Dr Naledi Pandor adayamikira WOMEN pokhazikitsa manifesitoyo.

“Manifesitowa ndi dongosolo lozama lofotokoza zomwe amayi a m’dziko muno akufuna.

“Mukawerenga modekha mumva kuti amayi akufuna akhale aphungu a Nyumba ya Malamulo, nduna za boma, komanso kutenga nawo gawo m’madera onse achitukuko,” adatero a Pandor.

Katswiriyu adaunikira mozama moyo wa Charlotte Maxeze, mayi wodziwika bwino pa nkhani yomenyera ufulu ku South Africa ndi kuwalimbikitsa amayi m’dziko muno kuti achilimike pofuna kukwaniritsa ufulu wawo.

A Kathewera Banda: Andale ayigwiritse ntchito

A Pandor ndi mphuzitsi, akhalapo nduna ya boma m’dziko la South Africa, komanso kazembe wa amayi ku United Nations.

Mkulu wa bungwe la Women Legal Resource Centre (WOLREC) a Maggie Kathewera-Banda akuti manifesito ya amayi ndi dongosolo lakuya la mfundo zomwe amayi akufuna zikwaniritsidwe kuti moyo wawo pa ndale ndi pa chitukuko usinthe.

Mkulu wa bungwe la Oxfam a Lingalireni Mihowa adati manifesito yoyamba idapangidwa mu 2018 koma idakhazikitsidwa mu 2019.

“Taganiza zoyisintha ndi kuyikhazikitsanso kaamba ka kusintha kwa zinthu m’dziko muno komanso m’maiko ena,” iwo adatero.

Manifesitoyo ikuunikira ufulu wa amayi wochita ndale, kukhala ndi katundu, malo, kugwira ntchito zofanana ndi abambo ndi zina zomwe WOMEN ikufuna atsogoleri ndi zipani zawo za ndale ziwunike mozama pamene zisankho za pa 16 Sepitembala zikuyandikira.

“Tikufuna atsogoleri a ndale ndi zipani zawo ayike m’manifesito awo mfundo zomwe zili m’manifesito a amayi n’kutiuza momveka zomwe adzachite akasankhidwa pofuna kukwaniritsa mfundozo.

“Tikufuna zofuna za amayi zidziwike ndi aliyense. Pamapeto pa zonse tikufuna kuona amayi akutenga gawo m’madera osiyanasiyana a chitukuko,” atero a Kathewera Banda.

WOMAN yapangidwa ndi mabungwe osiyanasiyana monga a Oxfam, Women Legal Resource Centre (WOLREC), Gender-Coordination Network, Hivos, UN ndi ena ambiri

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button