Chichewa

‘Yunifolomu ya polisi idamukhala’

Padali pa 14 June 2017 pomwe Richard Chitsamba adamuona koyamba mkazi wake Fosina Vasulu.

Apa nkuti awiriwo akuweruka m’zintchito mwawo ku Kanengo komwe Chitsamba amagwira ku kampani ya Limbe Leaf Tobacco pomwe Vasulu amagwira adali wapolisi pa Kanengopo.

“Vasulu adali ali muyunifolomu yake ya polisi ndipo ine ndidali ndi anzanga. Koma titamuona, tonse tidangolankhulira pamodzi kuti mkazi uyu yunifolomu yamukhala. Koma ine ndidanena kuti na uyu ndikwera minibasi yomwe akwerwe mpaka ndikadziwe kwawo,” adalongosola Chitsamba.

Mwatsoka, anzake a Chitsamba adamubwenzera mmbuyo pomuuza kuti wapolisi samufunsira atavala yunifolomu koma amadikira akavala zovala zina ati chifukwa akadatha kumumanga.

Komatu Chitsamba sadabwerere mmbuyo ndipo adamutsatira Vasulu mpaka m’minibasi yomwe adakwera.

“Ndimathokoza mnzanga Thokozani Kanzota yemwenso adandilimbikitsa kupita ponena kuti nanenso ndidali nditavala yunifolomu ndipo adandiperekeza mpaka tidakwera minibasi limodzi ndi Vasulu,” adatero Chitsamba.

Mwamwayi Chitsamba adakhala pampando umodzi ndi Vasulu ndipo adayamba kumuchezetsa mpaka kumupempha kuti amulipilire ya minibasi zomwe

zidathekadi.

“Titatsika ndidamufunsa nambala yake ya lamya ya m’manja yomwe ngakhale adavuta, adapereka ndithu,” iye adatero.

Komatu Vasulu ankati Chitsamba akamuimbira, amapereka lamyayo kwa mnzake kuti ayankhe zomwe iye zimamuipira.

Patadutsa nthawi, Vasulu adadzagwa m’chikondi ataona kuti Chitsamba samafuna zongosewera.

“Tsiku lina nditamuimbira adandiuza kuti akubwera ndimperekeze kumsika wa ku Nsungwi chakumadzulo ndipo m’malo mokwera basi tidayenda wapansi. China chomwe chidandipangitsa kuti ndidziwe kuti na uyu ndi wanga ndithu n’choti tidagwirana mkono mpaka kukafika kumsika opanda kukayikirananso kuti mwina tikumana ndi mbola ya mnzake,” Chitsamba adalongosola.

Vasulu akuti kutalika kwa Chitsamba ndiko kudamutenga mtima.

Patadutsa zaka zitatu awiriwo ali pa ubwenzi, adachita dongosola la ukwati ndipo pa 1 August 2020 adamangitsa ukwati wawo pa Nsungwi CCAP mumzinda wa Lilongwe.

Komatu awiriwo sadangofika pokwatirana ayi, adakumana ndi zokhoma monga Chitsamba kuuzidwa kuti apolisi ndi oyendayenda pomwe naye Vasulu ankauzidwa kuti anyamata a ku fodya nawo ngoyendayenda.

Iwo akulangiza anthu kuti mkazi wachisilikari naye ndi munthu ndipo amafuna chikondi chifukwa waona momwe mkazi wake amamukondera.

Pakadalipano awiriwo akukhalira ku ku Area 25B mumzinda wa Lilongwe.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button