Chichewa

Za mafumu m’matuni ndi m’mizinda

Listen to this article

 

Kalata yangayi ndikulemba kubwereza zomwe nthawi ina patsamba lomwe lino ndidadandaulapo zokhudza maufumu a m’mizinda ndi m’matauni. Lero ndabweranso kupempha boma kuti libwere poyera popanda kuzengereza kutiuza kuti maufumu alipo m’malokeshoni athuwa ndi m’mapuloti kapena ayi zinthu zisanafike poipa.

Mfumu ya mzinda wa Blantyre: Noel Chalamanda
Mfumu ya mzinda wa Blantyre: Noel
Chalamanda

Monga mumzinda wa Blantyre muno, chomwe ndikudziwa ndi choti a Malawi Housing Corporation ndi omwe amagawa nyumba kapena mapuloti kwa amene apeza mwayi panthawiyo. Si mfumu imene imagawa nyumba kapena puloti. Lero lino kwabadwa mafumu amene akuika anthu m’malokeshoni ndi m’mapuloti muukapolo.

A boma adziwe kuti mafumuwa akhazikitsa timalamulo tozunza komanso kuba monga kukalipira ndalama pamene mukukapereka uthenga wa maliro (mabanja a ku Chimwankhunda mumzinda wa Blantyre amalipira K3 000 ena mpaka K4 000 kwa mfumu Zingwangwa). Tangoganizani, ndi mabanja angati amene aferedwa ndipo akusowa kuti athandizidwe? Khansala wa derali akudziwa bwino za nkhani imeneyi.

Chomwe ndikudziwa ine ndi choti mfumu ya mzinda uno ndi Mayor ndipo amathandizidwa ndi makhansala amene timasankha m’mawodi athu. Za mafumuzi ine sindikugwirizana nazo chifukwa cha kusokoneza. Mafumu kumudzi, osati m’tauni muno.

  1. Mzunga,

Limbe, Blantyre

Related Articles

Back to top button