Chichewa

Zaka 14 kaamba kovulaza mkazi wake

Listen to this article

 

Juliyasi Dalasoni wa m’mudzi mwa Zidana, T/A Phambala m’boma la Ntcheu, amulamula kupita kundende kukagwira ukaidi kwa zaka 14 kaamba komenya ndi kuvulaza mkazi wake, Selina Juliyasi, modetsa nkhawa.

Malinga ndi umboni womwe udaperekedwa ndi apolisi m’bwalo la milandu la majisitireti la Lilongwe, izi zidachitika pa 26 December 2015, kwa Biwi mumzinda wa Lilongwe.

Khoti lidamva kuti mnyamata wina adathamanga kukadziwitsa Christina Walasi kuti mng’ono wake, Selina, wavulazidwa koopsa ndi mwamuna wake. Ndipo Walasi mothandizana ndi anthu ena adamutengera kuchipatala cha Kamuzu Central komanso kudziwitsa apolisi.

Our cartoonist’s impression of GBV
Our cartoonist’s impression of GBV

Lipoti la kuchipatala lidaonetsa kuti, Selina, yemwe akuti adamuwaza madzi otentha kunkhope komanso kumupondaponda pamimba mpaka kukomoka, adavulala kwambiri m’mutu, kunkhope kudzanso kuthyoka nthiti.

Selina mpaka pano akulephera kukhala pansi, kuyankhula komanso kudya kaamba ka ululu.

Ndipo patsiku lozenga mlanduwu posachedwapa, bwalolo litamufunsa kuti ndi chifukwa chiyani iye adachita chiwembu choterechi kwa mkazi wake, Dalasoni, wa zaka 45, adayankha kuti mkazi wakeyo adamugwira akuchita chigololo ndi mwamuna wina, zomwe zidamuwawa kwambiri.

Podziteteza Dalasoni adafotokoza motere: “Udali usiku wa pa 26 December 2015, pamene anthu adandiuza kuti akazi anga ali ndi mwamuna, choncho ine nditapita ndinakawapeza akupanga chigololo ndi mwamunayo. Atandiona mwamunayo adathawa, wamkazi adangophimba kumaso.

Nditawafunsa akazi anga kuti mukupanga chiyani, iwo anandigenda ndi njerwa ndi kundimenya, choncho inenso ndinawamenya ndipo adakomoka, ine ndinangochokapo zitatero.”

Koma atamufunsanso kuti abweretse umboni ooneka ndi maso pazomwe akunenazo, iye adangoti kukamwa pululu kusowa choyankha.

Pachifukwachi, wapolisi Euginio Yotamu, adapempha bwalolo kuti Dalasoni ayenera kulandira chilango chokhwima zedi kaamba kakuti mlandu womwe adapalamulawo ndi waukulu malinga ndi gawo 235 la malamulo ozengera milandu m’dziko muno.

Related Articles

Back to top button