Chichewa

Zitukuko pa Wenela

Listen to this article

 

Nyengo yasintha abale anzanga. Chikuchitika nchiyani? Pano pa Wenela, usiku winawo kudatentha zedi moti usiku onse ndimangokhalira kudzikanda.

Kutembenuka ndiye kudali kosayamba, thukuta lili kamukamu! Koma kungocha, mphepo idali kuomba moopsa, mosasula madenga. Ndipo tsiku linalo kudazizira ngati wafikanso mwezi wa June!

Chikuchitika nchiyani?

Lero kumva kuti kwina mphepo ya mkuntho yasasula madenga, kenako kumvanso kuti kwina mphenzi yapha anthu. Chavuta n’chiyani.

Tidakhala pa Wenela tsiku limenelo kudikira Moya Pete ankati adzatsegulire chitukuko china. Tonse tidakonzeka, kuitanitsa gologolo, amayi a chisamba aja lero asintha makaka kuchoka ku Polisi Palibe kupita ku Dizilo Petulo Palibe. Eyatu, zaka 51 za kuvina! Gogo ujatu adatipeza tikuvina ndiye mungaletse ndani kuvinira Moya Pete? Iye walakwanji kuti tisamuvinire?

art

Adafika Moya Pete ndi mdipiti wa galimoto zochuluka. Adabwera ndi anzake ambiri, pajatu ali ndi abwenzi ochuluka.

Adati tilowoloke njanji, nkumalowera kanjira kachidule kopita ku Mbayani. Tikuyenda chomwecho, tidapeza liboni lomwe amaika kusonyeza kuti pakutsegulidwa chitukuko.

“Ndayamika kwambiri, abale anzanga, lero lino tikutsegulira msewu umenewu kwambiri. Gogo uja palibe chimene adapanga pano pa Wenela kwambiri,” adatero Moya Pete.

Abale anzanga, kodi nkhani zotsegula mipita imeneyi nkuchita kutulutsa munthu wamkulu kuchoka kunyumba yachifumu ija adamanga gogo uja.

“Ndikuuzeni kwambiri. Male Chauvinist Pigs siyidzatiuza zochita pano pa Wenela. Mbamba ndikunenetsa kwambiri. Ndipo posachedwapa, ndikatsegulira gawo la msewu wa ku Amwenye ku Limbe,” adaonjezera chomwecho.

Abale anzanga, sindikudziwa za inu koma ndisaname, zimandivuta kumvetsetsa zinthuzi. Zili ngati Adona Hilida kunena kuti akulephera kubwerera pano pa Wenela chifukwa palibe wawapatsa nyumba. Kodi zaka zonse ankagawa abakha ankagona mumtengo?

Nchifukwa chake nanenso ndidavomereza mawu a Moya Pete kuti momwe zinthu zikukhalira pano pa Wenela, ndithu ana obwera mtsogolo adzatitemberera.

“Pano pa Wenela pakufunika anthu a maganizo ngati Che Guevera, Nelson Mandela ngakhalenso Fidel Castro. Kupanda apo, tipitiriza kuchemerera otsogolera kusolola akatchula dzina la Mama Tuge,” adatero Abiti Patuma titafika malo aja timakonda pa Wenela.

Musandifunse kuti amatanthauza chiyani chifukwa sindikuyankhani. Ndipo mukadziwa mukufuna mutani? Kapena mukathandiza kuchotsa miyala yokongoletsera Clock Tower?

Zonse zili apo, uyu mbale Fula Kasamba anthu amupana. Zoona mpaka kumukaniza kupita kwa sing’anga! Nthawi yowawitsa! Zinthu zimasintha!

Gwira bango, upita ndi madzi!!n

 

Related Articles

Back to top button