Chichewa

Kodi Chipuwa wabwerera kumalonda?

Listen to this article

 

Luso la Richard Chipuwa, goloboyi wa Flames komanso Mighty Be Forward Wanderers ndi losayamba. Pa 15 January chaka chino adachoka m’dziko muno ulendo ku Mozambique koma sadapatsidweko mwayi wosewera mpaka wabwerera kumudzi sabata yathayi. Kodi zatani? Msika wasowa? BOBBY KABANGO adacheza naye kuti amve zambiri motere:

Manja antchito: Chipuwa akuti ayese nawo ku Wanderers
Manja antchito: Chipuwa akuti ayese nawo ku Wanderers

Kodi mwabwera, mfumu?

Tafikatu amwene, tasowanatu koma mfumu.

Mwalemeratu, mpaka mwabwera ndi galimoto?

Hahaha nanunsotu musayambe apa…

Mwafika liti, mfumu?

Sabata yathayi, koma ndilipo chifukwa ndikufuna ndisewere m’dziko momwemuno kwa chaka chino ndipo ndibwerera chaka chamawa.

Ku Mozambique kwataninso? Mwathawa nkhondo kapena?

Ma documents ondiloleza kusewera mpira kumeneko sakuoneka mu system. Federation ya ku Maputo idandiuza kuti ma documents sakuoneka ngakhale Wanderers idatumiza. Izi zapangitsa kuti Chingale FC isandigwiritse ntchito. Chichokereni muja palibe chatheka ndiye ndaganiza kuti ndibwerere kumudzi kaye.

Vuto n’chiyani kuti asaoneke?

Nanenso sindikumvetsa, koma Wanderers idanditsimikizira kuti yatumiza.

Osati wathawa nkhondo?

Hahaha! Mayazi, amwene, sizikukhudzananso.

Ukutanthauza kuti sumasewera chichokereni kuno?

Ayi ndithu, ngati ndimasewera ndi magemu opimana mphamvu komanso ku training.

Apa simwatheratu, mfumu? Mumaka koma?

Ndine wampira, ndimadziwa ntchito yanga ndipo kupatsidwa mpata muonanso, mfumu.

Panopa ndiye ulowera timu iti?

Ndikufuna ndikambirane ndi Wanderers, zikatheka mwina ndisewera kumeneko. Zikakanika ndiye ndisewerera timu iliyonse yomwe timvane.

Komatu pochoka zimamveka ngati mwakangana ndi a Wanderers…

Ayi, padangokhala kusamvetsetsana koma zonse tidakambirana.

Uli ndi contract ndi Wanderers?

Ayi, moti tikamvana ndiye ndisayinira contract yatsopano koma ithe chaka chamawa. n

 

Related Articles

Back to top button
Translate »