Category: Chichewa

Cama ikuti zionetsero pa 17

Pamene nkhani yochita zionetsero pokwiya ndi utsogoleri wa Pulezidenti Joyce Banda mmene akuyendetsera dziko lino, ena mwa Amalawi otumikiridwa ati sakuona kuti kuyenda pamsewu…
‘Khirimasi idali yovuta’

Lachiwiri lidali tsiku la Khirisimasi, ndipo anthu adali kalikiliki kugula katundu kuti asangalale ndi mabanja awo tsiku lokumbukira kubadwa kwa Yesu Khristulo.
JB achotsa Kachali ku EC

Mtsogoleri wa dziko lino Joyce Banda wabweza moto, ndipo wachotsa wachiwiri wake Khumbo Kachali pampando woyang’anira bungwe la chisankho la Electoral Commission (EC).
Kapito adzudzula kukweza mitengo

Patangotha sabata bungwe la Malawi Energy Regulatory Authority (Mera) litakweza mitengo ya magetsi ndi mafuta agalimoto, madera ena maka kumidzi zinthu akuti zayamba kale…
Aimika malamulo a mathanyula

Mafumu ndi a mipingo ena adzudzula zomwe idanena nduna ya zamalamulo m’dziko muno, Ralph Kasambara kuti boma layamba laimika malamulo oletsa mchitidwe wa mathanyula.

Amuna ambiri amakonda zongotenga asungwana osawadziwa n’kukagona nawo ku maresitihausi. Zikatha bwino, amaoneka wochenjera. Komatu amaiwala kuti nthawi zina akhoza kugwa nazo m’mavuto oopsa.
Zokhoma pa makuponi

Ndondomeko ya fetereza wotsika mtengo [wa makuponi] chaka chino m’madera ena monga Dedza, Karonga, Zomba komanso Kasungu yatsimikizika kuti magulupu ndi nyakwawa sakulandira nawo…