Chichewa

Bzalani mbewu zocha msanga—Lipita

Listen to this article

 

Woyendetsa ntchito za ulangizi ndi njira zamakono za ulimi muunduna wa zamalimidwe, Wilfred Lipita, wati alimi akuyenera kutengerapo phunziro pa zomwe zidaoneka muulimi wa chaka chatha ndi kusankha mwanzeru mbewu zolima chaka chino.

Polankhula ndi Uchikumbe paulangizi, Lipita adati masiku ano n’kovuta kutchera kuti mvula iyamba lero ndipo idzatha mawa mmalo mwake njira yabwino n’kusankha mbewu zocha msanga.

“Upangiri wa zanyengo ndi umenewo komanso payekha mlimi ayenera kukhala wozindikira kumwamba kukhoza kusintha nthawi iliyonse malingana n’kusintha kwa nyengoku,” adatero Lipita.

Lipita: Alimi ena apulumukira chinangwa
Lipita: Alimi ena apulumukira chinangwa

Iye adati kunjaku kuli mbewu zocha msanga zomwe mvula itati yadulira panjira, mlimi akhoza kupeza popumira kusiyana n’kukakamira mbewu zokhalitsa m’munda chifukwa izi ndizo zingalowetse njala.

Mkuluyu adatinso pomwe alimi akubzala mbewu zachizolowezi monga chimanga, nyemba, fodya ndi zina ayeneranso kulingalira za mbewu zina zopirira kuchilala monga chinangwa ndi mbatata.

Mu ulangizi wake, Lipita adati alimi ena chaka chino apulumukira chinangwa ndi mbatata kupatula ulimi wa mthirira malingana nkuti ulimi chaka chatha sudayende bwino chifukwa cha mvula yokokolola ndi ng’amba.

“Mbewu ngati chinangwa zili m’gulu la mbewu zomwe timati zachitetezo chifukwa ngakhale mvula idule, izo zimaberekabe. Palibe kanthu kuti mitsitsi yake ndi yaikulu kapena yochepa bwanji koma nkhani ndi yakuti mbewu zina zitakanika, mlimi amakhala ndi pogwira,” adatero Lipita.

M’madera ambiri chimanga chidatuluka ndipo mlangizi wamkuluyu adati imeneyi si nkhani yokhazikika pansi koma kulimbikira ntchito za m’munda monga kupalira kuti mbewu zisamalimbirane chakudya ndi udzu.

Iye adati mbewu zokulira m’tchire zimanyozoloka ndipo sizibereka bwino ngakhale mlimi ataononga ndalama zambiri kugulira feteleza.

“Omwe chimanga chawo chatuluka, ino ndiye nthawi yoyamba kulingalira kupalira ndipo chikafika m’mawondo ndi nthawi yothira feteleza wina ndi kubandira kuti chinyamuke ndi mphamvu,” adatero Lipita.

Iye adati chimanga chikanyamuka ndi mphamvu maberekedwe ake amakhala osiririka ndipo mbewu yake ikakhala yabwinonso, phesi limodzi limabereka chiwiri kapena chitatu podzakolola nkudzakhala ngati minda iwiri pomwe udali umodzi.

Kagwedwe kenikeni ka mvula ya chaka chino sikadadziwike chifukwa ngakhale m’madera ena mbewu zamera, ena mukadali mouma moti alimi sadabzalebe mbewu. Izi zikutsimikiza malangizo a mlangizi wamkuluyu kuti nzeru n’kukhala ndi machawi.n

Related Articles

Back to top button
Translate »