Chichewa

ANATCHEZERA

Listen to this article

Sapereka chithandizo

Agogo,

Ndine mtsikana wa zaka 21 ndipo ndili ndi mwana mmodzi. Amuna anga adandisiya ataona kuti ndili ndi pathupi ndipo mwana atabadwa adauzidwa koma mpaka pano sadabwereko kudzaona mwana wawo. Ndikawauza za chithandizo samayankha, amangozengereza. Chomvetsa chisoni nchakuti munthune ndimakhala ndi agogo okalamba poti makolo anga onse adamwalira. Ndithandizeni, ndipange bwanji?

Pepa mtsikana,

Apa zikuonekeratu kuti ngakhale ukuti ‘amuna anga’ anthunu simunali pabanja ngakhale mumagonana mpakana kuberekerana mwana. Chimene chimachitika nthawi zambiri n’chakuti atsikana akangogwa m’chikondi ndipo mwamuna akangowauza kuti awakwatira, basi amaganiza kuti mwamuna ndi yemweyo basi ndipo amayamba zogonana naye ati pofuna kulimbikitsa chikondi kuti asamakaike za chikondi chawo, kumene kuli kulakwa kwakukulu. Atsikana ambiri aononga tsogolo lawo chifukwa cha mchitidwe wotere chifukwa anyamata kapena amuna ambiri ndi akamberembere, ongofuna kudzisangalatsa osalabadira za tsogolo la mnzawo. Akangomva kuti mtsikana watenga pathupi basi, chibwenzi chimathera pomwepo. Zikatero mtsikana zako zada. Koma dziko lino lili ndi malamulo okhudza maukwati ndipo ngati wina wakuchimwitsa, ali ndi udindo woti akusamale komanso mwana. Ndiye apa usazengereze—pita ukadule chisamani kukhoti basi kuti chilungamo chioneke. Mwina amuna ena amene amakonda kuchimwitsa ana a eni akhoza kutengerapo phunziro!

Ndinamugwira chigololo

Anatchereza,

Ndakhala pabanja zaka 25 ndipo ndili ndi ana anayi. Mwatsoka tsiku lina ndidapezerera akazi akuchita chigololo ndi mwamuna wina koma adathawa kotero kuti sindidathe kumulanda china chilichonse ngati umboni ndipo pachifukwa ichi mlandu sudandikomere, amfumu adagamula kuti nkhani yanga ndi yopanda umboni choncho banja siliyenera kutha. Ine kubanjako ndidachokako koma mkazi wangayo akumapepesa kuti ndimukhululukire. Ndithandizeni, nditani pamenepa?

Achimwene,

Pepani ndithu kuti banja lanu lagwedezeka chifukwa cha kusakhulupirika kwa akazi anu. Kukhala m’banja zaka 25 si chapafupi ndipo kuti lero ndi lero banja lithe chifukwa choti wina wapezeka akuchita chigololo ndi chinthu chomvetsa chisoni zedi, makamaka chifukwa angavutike kwambiri ndi ana osalakwa. Kodi, achimwene, mumapephera? Ndafunsa choncho chifukwa ngati mumakhulupirira Mulungu, mawu ake kudzera mwa mwana wake Yesu Khristu, amatiphunzitsa za kukhululukira anzathu akatilakwira, osati kamodzi kapena kawiri kokha, ayi, koma maulendo 77 kuchulukitsa ndi 7 (77 x 7). Kodi inuyo mukufuna kunena kuti simudachimwepo ndi mkazi wina kapena mkazi wamwini chikwatirireni? Mwina mudachitapo chigololo koma simunagwidwe chabe! Ndiye apa, poti mkazi wanu wagwira mwendo kuti mumukhululukire, ine pempho langa ndi loti mutero ndithu, munthu salakwira mtengo, koma munthu mnzake. Ngati Mulungu amatikhululukira tikamuchimwira, ife ndani kuti tisakhululukire mnzathu akatilakwira? Mwachoka, kutali limodzi, chonde ganizani mofatsa. Komabe ndi mmene kunja kwaopsera masiku ano ndi mliri wa HIV/Edzi, ndi bwino ngati mungabwererane kuti mukayezetse magazi musanayambe kukhalira malo amodzi kuti mudziwe mmene m’thupi mwanu mulili. n

Related Articles

Back to top button
Translate »