Otenga mimba atagwiriridwa akhoza kuichotsa—Bwalo
Mtsikana yemwe adagwiriridwa ali ndi zaka 13 n’kupatsidwa mimba ndi bambo wa zaka 60 m’chaka cha 2022, Lachitatu adati adakhutira ndi chigamulo cha bwalo la milandu chomwe chidati boma lisinthe malamulo ndi kulola amayi ndi atsikana kuchotsa mimba zotere.
Mstikanayo, yemwe ali mu Sitandade 7 pa sukulu ina m’boma la Blantyre ndipo amangotchulidwa kuti AC pa mlanduwo adanena izi titamuyendera kwawo pa maso pa makolo ake. Kwawoko ndi mtunda wa makilomita pafupifupi 22 kuchokera pa bwalo la ndege la Chileka.

Woweruza milandu a Mike Tembo Lachiwiri udagamula kuti unduna wa za umoyo asinthe ndondomeko yochotsera pathupi ndi kulola amayi ndi atsikana amene achitiridwa nkhanza zotere ndipo akufuna kuchotsa mimba kuti akhoza kutero.
Mtsikanayo adati atamva za chigamulocho kuchokera kwa bambo ake, omwe amatchedwa kuti CJ pa mlanduwo, mtsikanayo adati mtima wake tsopano wakhala pansi.

“Ndipo dzulo ndinagona tulo tofa nato. Ndapeza mtendere,” adatero iye.
Mtsikanayo adasumira wa za umoyo pa chipatala chaching’ono cha Chileka a Jenala Solomon atakana kumuthandiza kuchotsa mimba imene idadza atagwiriridwa ndi a Lazaro Charles omwe adapezeka olakwa pa mlanduwo ndi bwalo la Chinsenjere ku Lunzu. Iwowa ali ku ndende komwe akugwira jere kwa zaka 14.
AC, yemwe ndi wachiwiri kubadwa m’banja la ana anayi, atsikana atatu, adasumiranso chipatala cha Chileka, Unduna wa za Umoyo komanso komishoni yoona za ufulu wa anthu ya MHRC.
Iye adapempha bwalolo kuti akuluakuluwo adaphwanya magawo 19 ndi 20 a zoona kuti pasamakhale kusiyana pakati pa amayi ndi abambo pa ntchito omwe amapereka ufulu kwa amayi ndi atsikana kuti azilandira chithandizo cha umoyo chokhudza kugonana ndi kubereka.
“Ndakondwa chifukwa amayi ndi atsikana atetezedwa. Pathupi pankandisokoneza maganizo ndipo ndi pempho langa kuti aphungu ndi mtsogoleri wa dziko lino achilimika potiteteza ku nkhanza zotere.
“Kunotu nkhani za mabanja a ana ndi zochuluka zedi moti anzanga ambiri amene ndidayamba nawo Sitandade 1 tsopano ali m’mabanja ndipo ndikudziwa asanu omwe ali ndi ana. Chonsecho palibe amene akumangidwa kaamba ka izi,” adatero iye.
Kadaulo wa za umoyo wa amayi, makamaka zaubereki ndi matenda a m’mimba pa chipatala cha Gulupu, adachotsa mimba ya mwanayo ndipo adauza bwalo kuti ngakhale chipatala cha Chileka chidakana kutero, mimbayo imaika pa chiopsezo cha umoyo ndi kaganizidwe kake.
“Poyamba ndinkafuna kudzakhala mphunzitsi, koma kenako ndidayamba kufuna udotolo. Koma pano, loto langa ndi lodzakhala woimira anthu pa milandu,” adatero iye.
Bambo a mwanayo, omwe ndi mlimi komanso amachita maganyu ndi kuchita bizinesi zazing’ono, adati adakhutira ndi chigamulocho chifukwa chidadzetsa mpumulo m’moyo mwawo.
“Zinkandiwawa kuti mwana asunge mimba yochita kukakamizidwa komanso ali wachichepere. Izi ndi nkhanza. Chinkandipweteka ndi choti mkulu adamugwirirayo ndi woyandikana naye nyumba ndipo ankamutuma mwanayu kuti azitunga madzi mkazi wake atapita kwawo kukalima. Ankadyerera maso pa mwanayu,” adatero bamboyo.
Nawo adapempha okonza malamulo kuti asinthe malamulo okhudza kuchotsa mimba chifukwa m’midzimu ndiye amayi ndi asungwana akufa kaamba kotsata njira za asing’anga pochotsa mimba.
Akazi awo, omwe adaperekera umboni m’bwalolo, nawo adati adakhutira ndi chigamulocho, ponena kuti mwana wawo, yemwe adapezeka ndi mimbayo bungwe lina litabwera kudzayeza ana a pa sukulu yake, amasautsika m’maganizo kaamba ka mimbayo.
“Adalekeratu kudya moti amangotupa kaamba ka kuganiza kwambiri. Adasiiratu kupita ku sukulu ndipo samasewera ndi anzake. Amayi m’midzimu akugwiritsa ntchito nthambi za chinangwa, masipoko a njinga ngakhalenso safu ndi mankhwala a asing’anga pofuna kuchotsa pathupi. Izi zimaika miyoyo pa chiswe n’chifukwa chake tidapita ku chipatala kuti akatithandize,” adatero iwo.
M’chigamulo chawo, a Mike Tembo adati kukanika kuthandiza mwanayo kuchotsa pathupipo potsata njira ya ku chipatala kudali kuphwanya magawo awiriwo monga adatambasulira Mayi Ireen Mathanga ndi Mayi Luntha Chimbwete omwe amaimira mwanayo.
“Khoti ili silikukaika kuti mtsikana amene wagwiriridwa ndipo watenga pathupi chifukwa cha nkhanzazo ali ndi ufulu wochotsa mimba popanda chiletso,” adatero iwo.
M’chigamulo chawo, a Tembo adati mwanayo apatsidwe chipepeo cha K3 miliyoni ndipo undunawo usinthe ndondomekozo pasanathe masiku 180.
Iwo adati pa mlanduwo zidaonekeratu kuti adindo adalephera kuteteza mwanayo.
A Godfrey Kangaude, mkulu wa Nyale Institute, bungwe lomwe lidapeza oimira mwanayo pa milandu adti adakhutira ndi chigamulocho.
“Tili ndi chikhulupiriro kuti Unduna wa za Umoyo utsatira zimene bwalo lanena pobweretsa ndondomekozi,” adatero iwo.
Mayi Chijozi, omwe ndi wapampando wa MHRC adati chigamulocho adachimva ndipo aona kuti pofunika kukonza ndi pati pofuna kupewa zotere.
Mtsogoleri wakale wa dziko lino Mayi Joyce Banda, m’chaka cha 2012 adakhazikitsa komiti ypadera imene mudali achipatala, odziwa za malamulo, a mipingo, mafumu, a mabungwe, nthambi za boma ndi ena kuti afufuze nkhani za amayi kufa kaamba kochotsa mimba m’chibisira.
Nthambiyo idalangiza kuti malamulo ochotsera mimba asinthe ndi kuonjezera kuti amayi amene agwiriridwa azipatsidwa mpata wochotsa mimba, ngakhalenso amene apatsidwa mimba ndi abale awo.



