Mpikisano pa usipikala, asankha nduna zina
Pomwe aphungu a Nyumba ya Malamulo ayambe kukumana posakhalitsapa, mpikisano ulipo pofuna kusankha masipikala ngakhalenso aphungu amene akhale m’makomiti.
Izi zili apo, mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika Lachinayi adaonjezera nduna zina ziwiri kuchokera pomwe adawalumbiritsa.

Malinga ndi kalata yochokera kwa mlembi wamkulu wa boma a Justin Saidi, a Mutharika asankha Mayi Rosa Fatch Mbilizi kukhala nduna ya za ulimi komanso chitukuko cha madzi ndi ntchito za mthirira pomwe a George Patridge ndi nduna ya za malonda, ntchito zokopa alendo ndi chitukuko cha mafakitale.
Awiriwa akuonjezera pa nduna zina zimene a Mutharika adasankha ndipo zidalumbiritsidwa kale. Iwowa ndi a Joseph Mwanamvekha omwe ndi nduna ya za chuma, a George Chaponda omwe ndi nduna yoona za ubale wa dziko lino ndi maiko ena komanso a Alfred Gangata omwe ndi nduna ya za m’dziko.
Aphungu 224 mwa 229 akuyenera kukalumbira pomwe Nyumba ya Malamulo ikhale ikukumana kuyambira pa 18 October, malinga ndi kalata ya mlembi wa nyumbayo Mayi Fiona Kalemba.
Malinga ndi kalatayo, aphunguwo akasankha sipikala pa 29 October, ndipo mtsogoleri wa dziko lino pa 31 October.
Padakalipano, zadziwika kuti anthu atatu, a Sameer Suleiman a chipani cha DPP, a Kondwani Nankhumwa a PDP ndi Mayi Catherine Mzumara ndiwo akapikisane pa mpandowu.
Izi zili apo, wapampando wa mabungwe woimira Amalawi Benedicto Kondowe ati udindowu ngofunika munthu wakupsa m’mutu.
A Kondowe omwenso ndi a katswiri pa za malamulo ati Nyumba ya Malamulo ndi gawo lalikulu ya kayendetsedwe ka dziko choncho oyendetsa nyumbayo akuyenera kukhala munthu wangwiro komanso opanda mantha alionse.
“Dziko limayenda m’malamulo omwe amapangidwa ku Nyumba ya Malamulo tsono mpofunika munthu wakupsa mmutu osangoti basi palowa mbewa ayi,” atero a Kondowe.
Posankha sipikala wa Nyumba ya Malamulo, aphungu amalosa maina nkupanga chisankho koma momwe zilili piano mpikisanowu uvuta kaamba koti chipani cholamula cha DPP chili ndi aphungu ambiri komanso chili ndi kandideti wake.
A Namkhumwa ati akufuna kubweretsa chikhazikitso m’Nyumba ya Malamulo momwe sipadzakhala chipani chophangira chifukwa Iwo akufuna Malawi osinthika.
“Ndidayamba ndale ndili ndi ndalama kale ndiye ena akamati ndikufuna udindo chifukwa cha ndalama n’kulakwa. Moyo wanga ndidapereka nsembe kwa Amalawi ndipo n’didzateteza ngakhale asakundifuna,’’ atero a Nankhumwa.
Aphungu omwe angosankhidwa kumene akuyembekezeka kudzasankha sipikala wa Nyumbayo pa 30 October 2025 koma kasakaniza wa m’nyumbayo akupeperera tsembwe.
“Tiyeni tipange zina m’dzina koma apapa awa ndi anzanga. Nidapita nawo ku chipatala Lamulungu. Ndikupatsani zakudya n’kumane kaye ndakazi anga atuluka kumene ku theater kuja.



