Jannah Theme License is not validated, Go to the theme options page to validate the license, You need a single license for each domain name.
Nkhani

A ‘blesser’ andipatsa mimba

Anatchereza,

Ndili ndi zaka 22 ndipo ndili ku sukulu ya ukachenjedwe chaka chachiwiri. Ine ndi wochokera banja losauka kwambiri.

Makolo anga ndi alimi ndipo chakudya sichikwananso pa khomopo. Ku mtundu kwathu palibe anapita ku sukuku. Ambiri ndi olekera ku pulaimale basi. Ine mwachisomo ndinakhonza bwino kwambiri maphunziro anga a Fomu 4 ndi pamene ndinasankhidwa ku koleji. Chifukwa cha kusowa, zimawavuta makolo anga kuti andithandize.

Nditaona kuti zikuvuta ndinapanga chibwenzi ndi abambo ena ake omwe ndi okwatira. Abambowa ndi aakulu zedi. Amandithandiza china chilichonse pa moyo wanga.

Chithandizochi chimakhala chochuluka kotero kuti inenso ndimatha kuwathandiza makolo anga kumudzi.

Ine ndapezeka kuti ndine woyembekezera. Nditawafotokozela abambowa andiuza kuti ndikachotse pathupipa. Nditafunsa chifukwa chake, iwo anati akula ndipo ali ndi matenda a HIV. Akutinso ndine msinkhu wa zidzukulu zawo za kumapeto.

Anatche, ine nditamva za matendazo thupi langa linagwidwa ndi tsemwe koopsa. Nthawi yonseyi sanandiuze kuti akumwa makhwala otalikitsa moyo.

Kuyambira tsiku limeneli ine ndikungooneka wodwala basi. Sindikudziwa kuti nditani. Mantha adzadza thupi langa lonse.

Ndikuona ngati ndifa mawa. Pano ndikufuna mimbayi nditaichotsa. M’kalasi palibe chomwe ndikumamva. Zanga ndi khawa basi.

Nditani ine Anatchereza?

Blantyre

Zikomo, mwana wanga! Kodi kusuluko simupatsidwa ngongole ya maphunziro ndi zakudya? Ngati mumapatsidwa ndiye kuti iweyo umalakwitsa kupanga chibwenzi ndi agogo ako.

Komanso uzindikire kuti ngati amakuthandiza mosefukira choncho, iwo amadziwa kuti m’thupi mwawo si muli bwino.

Iwe monga mtsikana wa ku koleji unayenera kuwauza abambowa pachiyambi kuti mukayezetse HIV musanayambe kugonana mosadziteteza.

Mwinanso unayenera kuwauza kuti muzidziteteza pogonana. Iwo zoti kuli matenda sumadziwa? Kapena zoti kuli makondomu sumadziwa? Chibwana chomwe umapangacho. Taonatu lero zakubwelera. Umasewera zende pa ulimbo.

Limba mtima izi zabwera basi. Pita kuchipatala kuti ukayezetse. Ngati matenda akupatsa chilandire ndipo uzimwa makhwala mwa ndondomeko yake.

Nkhawa zonse zitaye. Ngati uzikhala ndi nkhawa ufa msanga. Nkhawa ndi matenda amenewa zimadana. Mimba usachotse. Lera mimba imeneyo chifukwa wanyamula munthu. Ukachotsa ndi chimodzimodzi kupha.

Ndati ndichenjeze atsikana omwe muli ndi khalidwe limeneli. Dziwani kuti mumadzichepetsera moyo wanu. Azibambo omwe mumayenda nawo sangakuuzeni kuti ali ndi matenda chifukwa amakulipirani ndalama zambiri.

Moyo ndi mpamba usamaleni atsikana.

Anatchereza

Kuchipinda ndi zero

Azakhali,

Ndiuzeni zoona. Ndikuopa kuwafunsa abale anga chifukwa ndiyaluka.

Ine ndapangitsa kumene ukwati ndi mwamuna wanga. Chilowereni m’banja tikutha miyezi 4 koma sitinagonanepo. Kawirikawiri amabwera m’bandakucha.

Akafika amati atopa ndi ntchito. Pa chibwenzi tinakhala miyezi 6. Pa nthawiyo amati tisagonane chifukwa ndi uchimo kugonana musanamange banja. Lero tili m’banja sakuonetsa chidwi chofuna kugonana.

Nthawi zonse amati atopa. Ndili ndi zaka 23. Iwo ndi a zaka 29. Ndikamagona ndimakhala ndi zilakolako za amuna anga. Kodi banja limatero?

FK,

Machinga

Zikomo FK,

Eeeee pali ngozi pamenepo mwana wanga. Ngati n’kotheka pitani ku chipatala.

Umuuze mwa ulemu za ku chipatalazi. Ngati salola auzeni a nkhoswe msanga.

Limenelo ndi vuto lalikulu. Chomwe udziwe nchoti amuna amakonda chigololo kwambiri. Ndiye sizingatheke kuti mwezi yonseyi muzikhala osagonana.

Ulimbikire kwambiri kuti mupite ku chipatala. Kwinako akwawo amuthandize kuti zitheke basi. Ndikuganiza kuti makolo athandizilapo pamavuto amenewa.

Mwinanso unayenera kuwauza kuti muzidziteteza pogonana. Iwo zoti kuli matenda sumadziwa? Kapena zoti kuli makondomu sumadziwa? Chibwana chomwe umapangacho.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button