Abwekera ulimi wa nsomba

Kuweta nsomba za mitundu yosiyana ndi kopindulitsa chifukwa ambiri amazikonda. Kwa alimi a nsomba, phindu ndiye ndi la mnanu. HOLYCE KHOLOWA adacheza ndi mmodzi mwa alimiwa, Precious Kantande wa ku Mbulukuta m’boma la Zomba. Iwo adacheza motere:

Mudayamba bwanji ulimi wa nsomba?

Ndidayamba ndi kuweta abakha, nkhuku komanso mbira koma chidwi changa chinali pa ulimi wa nsomba. Nditatolera ndalama mu phindu la ziweto ndimawetazo ndi mmene ndidayamba ulimi wa nsomba munali mu 2010. Nsomba zimenezi zitakula kwa miyezi 6 ndinagulitsa ndalama zosachepera K200 000 zimene zinachititsa kuti ndikumbe dziwe lachiwiri limene ndidalisandusa nazale ya nsomba.

Kantande kuonetsa momwe amawetera nsomba zake

Dziwe lachiwirili nditakumba n’kuikamo nsomba zidaphanso makwacha ochuluka amene adandipangitsa kuti ndikumbe lina lachitatu pa mtengo wa K296 000 ndipo lachitatuli ndidalipanganso kukhala nazale ina ya nsomba.

Pakadalipano ndili ndi mayiwe anayi, awiri ndi manazale amene ndikuwetapo mbewu monga chilunguni ndi makumba zimene zikakula ndimaziyika m’mayiwe enawa kwa miyezi 6 kuti zikule ndigulitse ndi cholinga chakuti ogula azigula nsomba zimene akufuna.

M’mayiwemu mukuoneka abakha akuchitamo chiyani?

Abakha amenewa ndi ofunika kwambiri paulimi wa nsombawu. Choyamba amathira manyowa kudzera mu chitosi chawo chimene chikamira chimakafika pansi pa dziwe pamene pali zomera zimene nsomba zimadya komanso kubisalamo. Komanso abakhawa amathandizira kupha udzudzu ndi tizilombo tina.

Ndi phindu lanji limene mukupeza mu usodzi?

Ndamanga nyumba komanso ndikuchulukitsa ulimi wa ziweto monga mbuzi, mbira, abakha ndi akalulu.

Kuonjezera apo, nsombazi zikutithandizira kwambiri ku thanzi lathu. Mwachitsanzo, ngati kumunda sitinakolole zochuluka timapha nsombazi n’kukagulitsa ndi kugula chimanga ndi chakudya china chofunikira pakhomo pathu.

Loto lanu ndi lotani pa ulimi wa nsomba?

Ndikufunitsitsa nditakhala mmodzi wa alimi amene azidzatulutsa nsomba za mnanu m’dziko muno. Koma izi zikhoza kutheka malo anga ano akazungulilidwa ndi mpanda wa waya kuti zonse zizidzachitikira kumpandako.

Kupatula nsombazi ndikufuna ndipitirize kukuza ulimi wa ziweto popeza nsomba ndi ziweto zimadalirana. Mwachitsanzo, ndowe za ziweto timathira ku munda, tikakolola chimanga deya timadzathira pa dziwepa ngati chakudya kupangitsa kuti nsomba zizikula ndi thanzi.

Malangizo anu kwa amene ulimi wa nsomba amangowuopera kutali ndi otani?

Ulimi wa nsomba ndi waphindu chifukwa pakutha pa miyezi 6 iliyonse umayenera kutola chikwama basi chifukwa nsomba sizinama ukazisamalira bwino. Kotero, kwa amene akufuna kuyalula mphasa yawo ya umphawi kudzera mu ulimi wa nsomba asagwe mphwayi koma ayambe kuchitapo kanthu pompano osadikilira mawa pokumba mayiwe, kusankha mtundu wabwino wa nsomba, kusamalira bwino nsombazo komanso kusagwa mphwayi ngati sizikuyenda mu ulimiwu chifukwa chonona chifumira ku dzira.

Share This Post