Chichewa

Adona Hilida afika pa Wenela

Listen to this article

Adafika pa Wenela tsikulo Abiti Patuma akuimba nyimbo yatsopano ya Lucius Banda. Inde ija waimba ndi Thocco Katimba: Mwandikumbuka.

tadeyu

Yahwe, wandimasula

Wandimasula

Yahwe wandimasula

Wandipepesa

Yahwe wandipepesa

Nditi zikomo

Yahwe wandimasula

Ndinu patali….

Koma isanathe nyimboyo, wapamalo aja timakonda pa Wenela, Gervazzio, mnyamata wa ku Nkhotakota, adaika nyimbo ina ya mkulu wa kwa Sosola uja.

Kudali kuthyola dansi mkati mwa usiku. Musandifunse kuti nthawi idali bwanji chifukwa sindikuuzani. Ndipo mukadziwa mukufuna mutani? Idali nthawi yotaika basi.

Dansi ili mkati, mdima utafika pena, tidangoona kunja kukuwala ngati msana! Aliyense adanthunthumira.

Kutuluka panja, tidaona mzimayi ali palichero. Mzimayiyo adaponya nsalu imene idali paphewa pake pansi. Idali kufuka moto lawilawi ngati dziko la Malawi, dziko lamoto.

Tonse tidanthunthumira.

Posakhalitsa, ndegeyo idatera. Mayiyo adatsika.

“Osandiopa, ndine wanuwanu Dona Hilida. Mumati sindigabwere kuno kumudzi? Ndabwera kudzaona mbale wanga Pitapo. Mudziwa adandigawirapo mawiribala 50 mmbuyomu,” adayamba nkhani.

Mitima idakhalako pansi. Koma nanga munthu akafike pa Wenela pandege yausiku? Kodi kuchoka ku Zambia kufika pa Wenela kulibe basi? Izo zili apo, kudzera ku Zambia kuchokera ku Jubeki si kudzitalikitsa?

Ayi ndithu, abale anzanga, tizionera limodzi.

“Tsono bwanji mukubwera usiku chonchi? Nanganso bwanji mukubwera pamene mwana wanu Pitapo akufuna kuweruzidwa?” adafunsa Abiti Patuma.

“Mukumuzunziranji Pitapo? Simukuona akuzunzika?” adafunsa Adona Hilida.

“”Taonani momwe abambo ovala nkhwaira, amene amayi awo adamwalira kaamba kosowa mankhwala akuzunzikira pomunyamula pamachira aja adanyamulira Listonia Susi ndi Chuma kalelo,” adatero Abiti Patuma.

Koma, abale, inetu palibe chimene ndimatolapo pankhani zawozo. Kodi nanga ndidapondapo ku Nyumba ya Malamulo? Inetu Nyumba ya Chimfiti ku Zomba sindiyidziwa. Za Chingwe’s Hole, Emperor’s View ngakhalenso Mulunguzi Dam, inde koona nsomba za trout komanso mpandankhuku, ndimangomva mwa anthu.

“Koma mayi, simungachititse msonkhano masana pa Nyambadwe pompa? Kuchoka pano pa Wenela simungathe mphindi 10,” ndidatero.

Ndidaonjeza: “Mukadzangoti mwafika pa Chimsewu, ndidzakuimbirani nyimbo ija ya Adona Hilida! Wa-wa-wa-wa. Komanso: Tulutsani wanuyo, timuone, ngati si dona, ife wathu ndi dona!”

“Ngakhale ndikudziwa Moya Pete zikumulaka, nthawi yanga sinakwane. Mundiona ndibwera. Kugona kozizira ndakana. Inetu sangandipatse belo muja adachitira Kakali wathawa uja!” adayankha Adona Hilida.

Koma, abale, kunjaku kuli zigawenga. Zoona kuthawa belo! Koma Kakali! Ndikumvatu kuti mnyamata ameneyu si pano. Sachita nawo za mowa, koma amagulira ena mkati mwa usiku. Mwina timaona afika pa Wenela ngati sanalowere ku Zobue kukaletsa nkhondo ya Renamo.

Ndipo ndikumvanso mnyamata wa mandala ujanso adatchuka ndi zopezeka ndi foni ya m’manja ya malemu wophedwa naye amutulutsa. Nanga uyu wokaikiridwa kuombera Paulo Mwiyo mu Lilongwe kundende ya Chichiri amakachitanji?

Gwira bango, mbale wanga chonde, upita ndi madzi!n

Related Articles

Back to top button
Translate »