Nkhani

Adzudzula woswa mkazi ndi njerwa

yomwe ili m’dziko muno yomwe mtsogoleri wa dziko a Lazarus Chakwera adalengeza kuti yakhudza kwambiri maboma 23 mwa maboma 28 omwe ndipo pali chiyembekezo choti anthu oposa 5.7 miliyoni akhudzidwa kwambiri ndi njalayo.

Mafumu m’maboma osiyanasiyana akhala akupempha boma kuti lifulumile kutsegula misika ya Admarc kapena lichilimike kugawa chakudya m’madera mwawo chifukwa

Bamboyo adagenda mkazi wake ndi njerwa atamukaniza

Akuluakulu a zipembedzo adzudzula zomwe a Siyini Banda a zaka 29 anachita Lamulungu lapitali pomwe anamenya akazi awo ndi njerwa m’mutu pokwiya kuti sadawatsatire kuchipinda.

Bwalo la Nkhunga ku Nkhotakota lidamvetsedwa kuti a Banda ndi akazi awo amachokera ku kachisi kopemphera koma iwo atafika ku nyumba adawauza kuti awatsatire kuchipinda. Koma akazi awowo adapempha kuti aphike kaye chakudya, zomwe a Banda zidawanyasa ndipo adawamenya ndi njerwa m’mutu.

Pa bwalo la milandu a Banda adalamulidwa kupereka chipepeso cha ndalama zokwanira K100 000 apo bii amayenera kukagwira ukaidi koma anakwanitsa kupereka ndalamazo.

Mkulu woyang’anira za m’mabanja mu mpingo wa Seventh Day Adventist (SDA) m’dziko lino a Pastor Lonely Phiri adadzudzula mchitidwewu kuti ndi wosemphana ndi ganizo la baibulo komanso chikonzero cha Mulungu pokamba za banja.

Iwo adati: “Timalimbikitsa kuthana ndi nkhanza kwa anthu wonse a pa banja, amayi, atsikana komanso anyamata m’chilinganizo chomwe timakumbukira pa dziko lonse sabata ziwiri zapitazo chomwe m’Chingerezi timati End it Now. Tsono zachitika apazi ndi nkhanza chifukwa mayiyo amapereka chifukwa chokwanira. Komanso kugenda mkazi wako ndi njerwa ndi kuphatu kumeneko. Tsono akamupha thupi likatentha azipita kuti?”

Ndipo mbusa wa mpingo wa Jombo Souls Harvest Ministry m’boma la Chikwawa, Pastor Derrick Simenti anati baibulo limanena kuti mwamuna ndi mkazi adzasiya makolo awo nangakhala thupi limodzi molingana ndi Genesis 2:24 ndiye ndi zovuta kumvetsa kuti thupi limodzi lija likugendananso ndi njerwa.

Mneneri wa Muslim Association of Malawi (Mam) shehe Dinala Chabulika adati ichi ndi chitsimikizo choti kulolerana pakati pa awiriwa kunasowa.

“Zomwe zachitika ku banjalo ndi chitsimikizo kuti m’banjamo muli chimkulirano. Awiriwa sagwirizana chifukwa ngati pali kugwirizana sungamukanize mnzako pa chomwe akupempha komanso sungamuganizire mnzako zofuna kumumenya,” adatero a Chabulika.

Pophera mphongo, shehe Abdullah Shafi wa mzikiti wa ku Nsanje anati ngakhale kuti ndi ufulu woti mwamuna akhonza kukhala malo amodzi ndi mkazi wake, mwamunayo amayeneranso kukhala ndi udindo womuteteza mkaziyo.

Iwo anati: “Izi ndi nkhanza kwa mkaziyo chifukwa m’kumvetsetsa kwanga iye sakukana koma akufuna kuphika kenako akwaniritse zomwe mwamuna wake amafunazo. Mwamunayo amayenera adekhe kaye, potengera kuti chakudyacho amayenera kudya ndi iyeyo. Pajatu mu Genesis 2:18 – 19 Mulungu anaona kuti si kwabwino kuti munthu akhale yekha ndipo Admarcanamupangira womuthangatira. Tiyeni amuna wokwatirafe tizimvetsetsa akazi athu akatiyankhula makamaka pankhani zokhudza kugonana.”

Sheheyo adayamika bwalo kaamba ka chilangocho. “Tikaonetsetsa, mwinanso amayenera kumutumiza ku ndende komanso kukamuyeza ku chipatala cha anthu a vuto la za ubongo kuti aone ngati ali ndi kaganizidwe kangwiro apo biii tsiku lina akhonza kudzamupha mkaziyo. Koma izi Mulungu sakondwera nazo,” adatero a Shafi.

Kumbali yawo, mbusa wa mpingo wa Thundu CCAP mu mzinda wa Blantyre a Moyenda Kanjerwa nawo adazudzula bamboyo poti zomwe achitira mkazi wawoyo si uMulungu.

Iwo adati buku lopatuluka limalimbikisa chikondi kotero pongomenya mkazi pakusonyeza kuti uMulungu udawatalikira.

“Zomwe bambo mnzathuyu ndi mphamvu ya chiwanda chifukwa baibulo limatiphunzitsa kukhala okondana. Bukuli limalimbikisa abambo kukonda akazi awo ndipo amayi amalimbikitsidwa kuti azimvera amuna awo koma sadasonyeze kuti azichitirana nkhaza.

“Komanso bamboyu akungofunika kukhala naye pansi ndi kumupatsa malangizo a uzimu malingana ndi momwe angakhalire ndi a chikokndi ake,” adatero iwo.

Naye mtsogoleri wa African National Council of Bishops (Ancob) a Evans Khobidi adati mayiyo ndi pomwe ali olakwitsa pomukana mwamuna wake ku chipinda.

“Zimene munthu wa mayi anachita pokaniza mwamuna kukhala naye ndi zoletsedwa mumalemba chifukwa Paulo mtumwi analembera mabanja a ku mpingo wa ku Korinto pa 1 Akorinto 7:5,” adatero iwo.

Malembawo amati: “Musakanizane, koma ndi kuvomerezana kwanu ndiko, kwa nthawi, kuti mukadzipereke kwa kupemphera, ni mukakhalenso pamodzi, kuti Satana angakuyeseni, chifukwa kusadziletsa kwanu. Koma ichi ndinena monga mwa kulola, si monga mwa kulamulira.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button