Chichewa

Agundidwa akuthawitsa katundu wakuba

Listen to this article

 

Bambo wina wagundidwa ndi galimoto ku Mzuzu pomwe amathawitsa mapaketi awiri a khofi omwe amamuganizira kuti adaba pa Mzuzu Coffee Den.

Bamboyo, yemwe ndi Laston Kaunda wa zaka 32 ndi wochokera m’mudzi mwa Chiphanzi, T/A Nkumbira m’boma la Nkhata Bay.

arrest

Mneneri wapolisi mumzinda wa Mzuzu, Patrick Saulosi, adati mnyamatayo adapita ku Coffee Den m’mawa wa Lachiwiri sabata yatha ndi nsuweni wake komwe adakanyamula mapaketi a khofiwo.

“Woganiziridwayo akutuluka mu Coffee Den muja adatuluka ndi mapaketi awiri a khofi osalipira. Mnyamata wogwira ntchito pamalopo ataona zomwe amachita Kaunda adayamba kumuthangitsa,” adafotokoza Saulosi.

Saulosi adati pa nthawi yomwe Kaunda amafuna kuoloka nsewu galimoto idamuomba ndipo iye adavulala kwambiri mwendo.

“Iyeyo ali kuchipatala cha Mzuzu Central Hospital (MCH) koma akangotuluka kuchipatalako atengedwa ndi apolisi pamlandu wakuba,” adatero Saulosi.

Saulosi adati kaamba ka kuchepa kwa mlanduwo palibe wapolisi amene akudikirira Kaunda kuchipatala podikirira mlandu.

Msangulutso utapita kuchipatalako udakumana ndi Kaunda yemwe akadali m’chipatala kulandira thandizo.

Kaunda adati sakukumbukira chilichonse chomwe chidachitika patsikulo chifukwa adali ataledzera kwambiri.

“Sindikudziwa chomwe chidachitika ndidangozindira kuti ndili kuchipatala kuno,” iye adayankha motero.

Iye adati apolisi adabwerako kuchipatalako koma sadamuuze kalikonse

Related Articles

Back to top button
Translate »