Chichewa

Akhazikitsa kamtengo pachipatala cha nkhalamba

Listen to this article

Malingana ndi kuchuluka kwa anthu achikulire amene amabwera pachipatala cha anthu okalamba cha Kalibu Elderly Clinic ku Lirangwe m’boma la Blantyre, chipatalachi chaika kamtengo pa thandizo limene akupereka.

Malingana ndi mmodzi mwa madotolo a mafizo pachipatalacho, Veronica Mughogho, izi zithandiza kuti chithe kufikira anthu okalamba ochuluka kwambiri makamaka a kumidzi amene amasowa chipatala chawo chenicheni.

Mughogho: Okalamba kwambiri sazilipira

“Taika mtengo kwa achikulire okhawo amene sadapyole zaka 60 ndipo kwa iwo amene adapyola sazilipira kanthu. Ndalamayi ndiyochepa chabe choncho  ndiyoti anthu akumudzi akhoza kumalipira mosavuta,” iye adatero.

Chipatala cha Kalibu Elderly Clinic adachitsegulira zaka ziwiri zapitazo ndi cholinga chofuna kuthandiza anthu okalamba makamaka ku vuto kapena matenda okhudzana ndi mafupa amene anthu ambiri akamakula amakumana nawo.

Kupatula kuona odwala amene amabwera okha kuchipatalacho, madotolo ndi anamwino amayendera odwala m’nyumba zawo ndi kumakawathandiza.

Kuonjezera apo, ogwira ntchito pa chipatalachi amachititsa chipatala choyendayenda m’madera osiyanasiyana kuti ngati pali odwala ena achikulire kwambiri amene sangathe kubwera kuchipatala kaamba ka vuto la mayendedwe athandizike.

“Padakalipano sitidayambe kugonetsa anthu odwala pachipatalachi koma kutsogoloku tidzayamba. Tilinso ndi malingaliro ofuna kufikira matenda ena ochuluka,” adatero dotoloyu.

Related Articles

Back to top button
Translate »