Chichewa

Akwizinga ‘wogwirira’ wamisala

 

Apolisi ya Kanengo ku Lilongwe anjata bambo wa zaka 46 Nelson Chiudzu pomuganizira kuti adagwirira mai wa zaka 49 Maria.

Apolosi ati abale a mai ogwiririrayo adagwira Chiudzu akuchotsa ulemu maiyo n’kumutengera kupolisi ndipo akuyembekezera kukaonekera kubwalo la milandu kukayankha mlandu ogonana ndi munthu wamisala zomwe zimatsutsana ndi ndime 139 ya malamulo a dziko lino.

Mtambo: Zalakwika

“N’zoonadi tamumanga koma sitidapeze kuti cholinga chake chidali chiyani. Mlandu wake walembedwa kale moti nthawi iliyonse akaonekera kubwalo la milandu pa zomwe adachitazo,”  adatero mneneri wapoliasi ya Kanengo Laban Makalani.

Iye wati Chiudzu wauza apolisi kuti wakhala paubwenzi wamseri ndi mai wozungulira mutuyo kuyambira mwezi wa December 2017 ndipo ati samaona cholakwika chilichonse pazomwe amachitazo.

Mkulu oona za ufulu wa anthu Timothy Mtambo wadzudzula mchitidwewu chifukwa maiyo saganiza bwino ndipo akhoza kulola chilichonse osadziwa zotsatira zake.

“Ichi n’chifukwa chake boma lidakhazikitsa malamulo kuti munthu wa nzeru zake sangagone kapena kupanga ubwenzi ndi wamisala kapena mwana chifukwa sadziwa chomwe akuchita,” adatrero Mtambo.

Iye adati anthu alunga ali ndi udindo oyang’anira olumala omwe wamisala ali m’gulu ndipo ngati anthu alungawo akuyambitsa kuchita nkhanza anthu oyenera kuwaterewo, ndiye kuti miyoyo ndi ufulu wawo zili pachiopsezo.

Mtambo wati abale a anthu amisala akuyenera kukhala maso pa komwe m’bale wawoyo akupita kapena kulowera chifukwa anthu oyipa mtima amawapezerera komwe ali okhaokha chifukwa amadziwa kuti alibe mphamvu yokana chilichonse.

Mai Asina Rajab a m’boma la Salima ati nthawi zina nkhanza zotere siziyamba chifukwa cha chilakolako chokha komanso zikhulupiriro zomwe asing’anga ena amanamiza anthu ofuna kukhwima.

Iye adati munthu wamisala ali ngati mwana yemwe sangathe kudzisamalira yekha ngati mkazi ndiye zimadabwitsa kuti abambo ena amalimba mtima n’kumagona ndi munthu otereyo osalingalira za ukhondo wake ngati mkazi.

“Pamoyo wa mkazi pamachitika zambiri ndipo amayenera kudzisamalira mwapadera tsono zimadabwitsa kuti abambo ena saona zimenezi mpaka kumagona naye. Sichabe ayi koma pali zifukwa zina,”adatero Rajab.

Chiudzu amachokera mmudzi mwa Nyonyo mfumu yayikulu Chimutu Ku Lilongwe pomwe Mwera amachokera mmudzi mwa Limwera mfumun yaikulu Chimutu ku Lilongwe komweko. n

Related Articles

Back to top button