Chichewa

Alimi musaiwale mitengo ya chonde

Listen to this article

 

Bungwe lomwe limalimbikitsa alimi kubzala mitengo yosiyanasiyana la World Agroforesry Centre lapempha alimi kuti asaiwale mitengo ya chonde akamabzala mitengo chaka chino.

Woyendetsa pologalamu ya Agroforestry Food Security yomwe cholinga chake n’kuonetsetsa kuti alimi akukhala ndi chakudya chokwanira, Dr Bruce Sosola, adati kugwiritsa ntchito mitengo ya chonde kukhoza kuchulukitsa zokolola ndi katatu pamunda.

Mkuluyu adalankhula izi pomwe amayendera nazale za mitengo za alimi ku Lumbadzi Lachiwiri lapitali komwe adati ndi wokhutira ndi ntchito yomwe alimi akuchita pankhani yobwezeretsa chilengedwe.

Sosola adati ina mwa mitengoyi monga Gliricidia ikhoza kugwiritsidwa ntchito limodzi ndi mbewu monga chimanga pomwe ina imafuna kuibzala mwakasinthasintha ndi mbewu ndipo imatha kugwiritsidwa ntchito kwa zaka ziwiri kapena zitatu mlimi asanabzalenso ina.

Sosola kuyendera nazale ya mitengo yobwezeretsa chonde m’nthaka
Sosola kuyendera nazale ya mitengo yobwezeretsa chonde m’nthaka

“Kafukufuku yemwe tidapanga mmbuyomu adasonyeza kuti alimi akhoza kupindula kwambiri ndi njirayi chifukwa amalowetsa ndalama zochepa muulimi wawo. Pali mitengo ina monga ya Gliricidia yomwe mlimi akhoza kuphatikiza ndi mbewu monga chimanga popanda kusokoneza kakulidweka chimangacho.

“Mitengoyi imathandiza kubwezeretsa michere yachilengedwe m’nthaka. Komanso imagwira bwino kwa mlimi yemwe ali ndi malo ochepa chifukwa amabwezeretsa chonde m’nthaka pomweso akulima mbewu zake nthawi imodzi,” adatero Sosola.

Iye adati ubwino wina wa mitengoyi ndi wakuti imayamwa mchere wa Nitrogen ndi kuwusunga m’masamba ake ndi kuyamwanso mchere wachilengedwe womwe udathawira pansi ndi madzi nkuwubweretsa pamwamba kuti mbewu zizigwiritsa ntchito.

Kupatula Gliricidia, Sosola adati paliso mitengo ina monga katupe (Tephrosia), Sesbania, Cajanus komanso Faidherbia yomwenso imagwira ntchito yobwezeretsa chonde munthaka.

Iye adati mbewu yamitengoyi ndi yosavuta kupeza ndipo alimi akhoza kuipeza kudzera kumaofesi a bungweli omwe ali ku Chitedze Research Station ku Lilongwe pamtengo wotsika.

Iye adati bungweli limapereka upangiri kwa alimi omwe ali ndi chidwi chotsata njirayi momwe angachitire kuti apeze phindu lochuluka.

Adatinso ena mwa alimi omwe adawaphunzitsa kale pano adasanduka odziyimira paonkha ndipo akumagwiranso ntchito yophunzitsa alimi anzawo.

Mayi Dorothy Themba wochokera kwa Mpingu ku Lilongwe adathirira umboni kuti banja lawo lapindula kwambiri ndi njirayi. Iwo adati tsopano akukolola pafupifupi milingo itatu pa mbewu zomwe amabzala kuyerekeza ndi zomwe amakolola poyamba pamunda womwewo.

“Ndidazindikira mochedwa kuti njirayi ndi yopindulitsa kwambiri. M’chaka choyamba kugwiritsa ntchito njirayi zokolola zanga zidawonjezekera koma apa n’kuti mitengoyi isanayambe kugwira ntchitokwenikweni.

“M’chaka chotsatiracho ndidadzadza nkhokwe ziwiri zikuluzikulu ndi imodzi yaing’ono pomwe poyamba ndinkakolola nkhokwe imodzi yokha basi,” adatero Themba.n

Related Articles

Back to top button