Amalawi alankhula pa malonjezo
Amalawi ena ati mpofunika ndondomeko zogwirika kuti boma lomwe lalowa kumene la DPP likwaniritse malonjezo ake a m’manifesto.
Ena mwa malonjezo omwe Amalawi alankhulapo kwambiri ndi okhudza sukulu za sekondale za ulere komanso zokhudza fetereza.

Koma kutengera momwe zimayendera, ndondomeko zoyenerazo zikudikira kulumbira kwa aphungu a Nyumba ya Malamulo omwe ali ndi udindo wovomereza ndondomeko zomwe boma likufuna kugwiritsa ntchito.
Padakalipano, Nyumba ya Malamulo idatulutsa mndandanda wa zomwe zichitike kufikira aphunguwo adzalumbire koma tsiku lenileni silidadziwike.
Pounikira za maphunziro aulere m’sukulu za sekondale, kadaulo pa za maphunziro a Benedicto Kondowe wati kukhazikitsa maphunziro aulere m’sukulu za sekondale n’kolira bajeti yaikulu.
Iwo ati mpofunika kuonjera makalasi, kuphunzitsa ndi kulemba aphunzitsi ambiri ndi kuonetsetsa kuti zipangizo zophunzitsira ndi kuphunzirira zikupezeka.
“Tikufunika ndalama zoposa K67 biliyoni kuti maphunziro aulere m’sukulu za sekondale atheke. Tikatengera bajeti ya maphunziro yomwe imakhalapo n’kale, tikufunika kusakirapo mokhetsa thukuta,” atero a Kondowe.
Iwo aunikira kuti mwin njira yabwino ikadakhala kuwonjezera thumba la ndalama zothandizira ophunzira ovutikitsitsa.
Koma kadaulo winanso a Limbani Nsapato ati pulogalamuyo ikhoza kutheka patakhala ndondomeko yabwino monga kuyamba n’kumapereka K20 pa K100 iliyonse ya mubajeti ku unduna wa za maphunziro.
Pa za ulimi, pulezidenti wa bungwe la alimi la Farmers Union of Malawi (FUM) Mayi Mannes Nkhata ati mpofunika ndondomeko zoti alimi azitha kugula fetereza nthawi yabwino kuti ulimi uziyenda bwino.
“Ngatidi boma likufuna kutukula ulimi, likuyenera kukhala ndi ndondomeko zokhwima zomwe zizionetsetsa kuti m’nkhokwe zake za fetereza muzikhala fetereza wa chaka chinacho. Izi zizithandiza kuti kukonzekera kwa chaka chinacho kusamavute,” atero a Nkhata.
Mlimi wochokera kwa Dzoole m’boma la Dowa a Danniel Mtambo ati alimi amabwezeredwa mmbuyo kaamba kakuchedwa kwa fetereza komanso mitengo yomwe akakolola sapeza nayo phindu.
“Fetereza azipereka mwezi ngati uno wa October usadathe komanso mtengo uzikhala woganizira alimife. Ndife amene timadyetsa ngakhale mabwanawo kumeneko,” atero a Mtambo.
Naye mlimi wa kwa Chitukula m’mudzi mwa Mzinga a Christopher Nyamasauka ndi a Lyton Alfred ati ndondomeko yoti fetereza azipezeka chaka chonse njabwino chifukwa alimi masiku ano sadalira ulimi wa mvula wokha.
“Enafe timafuna fetereza chaka chonse chifukwa tikachoka kumunda, timapita ku dimba. Pena timaphatikiza ku munda ndi kudimba ndipo timadzapitiriza ndi ku dimba tikakolola zoyambazo,” atero alimiwo.
Mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika polankhula atalumbira adatsindika kuti ntchito yawo yoyamba ikhala kuonetsetsa kuti ntchito za ulimi zatukuka, ndalama zakunja zikupezeka, mafuta agalimoto akupezeka komanso adalonjeza maphunziro aulere a msukulu zasekondale.