Chichewa

Amayi apatsidwe mwayi pa ndale

Mabungwe a Oxfam ndi Women and Legal Resource Centre (WOLREC) akuthandiza amayi, achinyamata ndi anthu aulumali omwe akufuna kudzapikisana nawo pa zisankho za pa 16 Sepitembala 2025. MACMILLAN MHONE adacheza ndi mkulu wa bungwe la Oxfam a Lingalireni Mihowa kuti amve zambiri:

Tafotokozani mwachidule ntchito zokhudza zisankho za pa 16 Sepitembala 2025 zomwe mabungwe a Oxfam ndi WOLREC akugwira.

Malamulo a dziko lino amati amayi ali ndi ufulu wokwaniritsa zofuna zawo pa ndale. Tilinso ndi ndondomeko zolimbikitsa utsogoleri wa amayi pa ndale. Kwa zaka zingapo, takhala tikupanga kampeni yolimbikitsa amayi kutenga nawo gawo pa ndale yotchedwa 50:50. Pamene tikuyandikira zisankho za mu Sepitembala chaka chino, tikupereka upangiri wothandiza amayi omwe akufuna kuima nawo pa mipando ya ukhansala ndi uphungu wa ku Nyumba ya Malamulo.

Mihowa:: Chiwerengero cha amayi, achinyamata ndi anthu aulumali chikwere

Kodi n’chiyani chomwe mukufuna kukwaniritsa?

Tikufuna kulimbikitsa amayi kuima nawo pa zisankho za mu Sepitembala, komanso kukhala patsogolo pa ndale. Tikufuna kukwaniritsa ndondomeko yomwe boma la Malawi lidakhazikitsa yoti mwa makhansala ndi aphungu 100 alionse omwe adzasankhidwe, 35 adzakhale amayi.

Mwakhazikitsa ndondomeko zotani zothandiza kukwaniritsa zolinga zanu?

Mu 2023, ifeyo a Oxfam ndi a WOLREC tidakumana ndi amayi omwe akufuna kulowa ndale ndipo adatiuza kuti akusowa upangiri kuchokera kwa amayi omwe ndi mkhalakale pa ndale. Adatipatsa maina a amayi omwe amafuna kuti adzawapatse upangiriwo. Pachifukwa ichi, m’maphunziro omwe takhala tikuchititsa takhala tikuitana mkhalakale pa ndale monga a Patricia Kaliati, Mary Navicha, Catherine Gotani-Hara, Esther Jolobala ndi a Rachel Zulu kuti asule amayi anzawo.

Ndi magulu ati omwe akuyembekezera kupindula ndi ntchitozi?

Maphunzirowa tikupereka kwa amayi omwe akufuna kudzaima nawo pa mipando ya ukhansala ndi uphungu wa ku Nyumba ya Malamulo.    

Kodi iwowa apindula motani?

Amayiwa akulandira upangiri kuti kudziwe zinthu zofunika pa ndale, komanso zoyenera kuchita kuti adzapambane pa zisankho za pa 16 Sepitembala. Amayi omwe adzalandire chiphaso kuchokera ku bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) chowalola kudzapikisana nawo pa zisankhozo, tidzawapatsa zinthu zowathandiza kuchititsa misonkhano yokopa anthu. Tikuyetsetsa kuti amayi tawafikire kwa nthawi yaitali.

N’chiyani chomwe amayi akuyenera kuchita kuti apindule nawo?

Padakali pano Oxfam ndi WOLREC akulangiza amayi kuti akhale olimba mtima, odziwa kucheza ndi anthu a m’madera mwawo, komanso tikuwapatsa luso la mmene angadziwire zofuna za anthu, komanso ukadaulo wapadera wa mmene angaperekere mauthenga okopa anthu m’misonkhano yawo.  Mabungwewa athandizanso amayi kudziwa malamulo oyendetsera zisankho a dziko lino kaamba koti adasintha.

Mukugwira ntchito motani ndi bungwe la MEC?

A MEC tidawafotokozera zomwe tikuchita ndi zolinga zake ndipo adatipatsa chiphaso chotilola kumemeza anthu pa nkhani zokhudza zisankho, komanso kuyendera malo oponyera voti.

Tidakumananso ndi wapampando wa MEC a Annabel Mtalimanja n’kuwapempha kuti ndalama zomwe amayi amalipira ku bungwe lawo akafuna kupikisana nawo azitsitse ndipo pempho lathu lidamveka kaamba koti amayi apereka ndalama zocheperako poyerekeza ndi abambo.

Ndi ntchito ziti zomwe mabungwe anu akwaniritsa kale?

Tachititsa kale maphunziro a amayi m’zigawo zonse za m’dziko lino. Tafikira mafumu n’kuwapempha kuti alimbikitse amayi a m’madera awo kuti atenge nawo gawo pa ndale. Tachititsa misonkhano ndi amayi, apolisi ndi atsogoleri azipembedzo zosiyanasiyana.

Rwanda, South Africa ndi Namibia ndi ena mwa maiko omwe akuchita bwino poonetsetsa kuti amayi akutenga nawo maudindo a ndale. Kodi anzathuwa adagwiritsa ntchito ndondomeko zotani zoti ife tiphunzire nawo?

Maiko a anzathuwa amaperekeratu mipando ina kuti ikhale ya amayi. Kutsogoloku dziko la Malawi likufunika liikenso ndondomeko zofanana ndi za anzathuwa. M’mbuyomu nkhaniyi idakambidwapo koma siidafike popanga lamulo loti aphungu a ku Nyumba ya Malamulo aliunike. Pachifukwa ichi, tikuthamangabe pogwiritsa ntchito malamulo omwe tili nawo.

Tafotokozani mwatsatanetsatane mavuto omwe amayi akukumana nawo.

Akusowa upangiri wa mmene angachitire kampeni, ndalama zolipira pa zisankho, komanso ziwawa zikubwezera mmbuyo ntchito yolimbikitsa amayi kutenga gawo pa ndale. Amayi akukumana ndi zotsamwitsa zosiyanasiyana pa zisankho za chipulula za m’zipani.

Mukuthana nawo bwanji mavutowa?

Takhala tikukumana ndi zipani kuti apange ndondomeko zoti amayi asapsinjike pa zisankho za chipulula. Ndife okondwa kuti zipani zina zidamvera ndipo zidaika ndalama zocheperapo zoti amayi azilipira akafuna kuimira.

Pa nkhani ya ziwawa, takhala tikukambirana ndi atsogoleri a zipani za ndale, komanso mkulu wa polisi a Merlyne Yolamu kufunika kopeza njira zothetsera ziwawazo. Amayi omwe akufuna kudzaima pa zisankho za pa 16 Sepitembala adawafotokozera a Yolamu mavuto omwe akukumana nawo ndipo iwo adalonjeza  kukhazikitsa komiti yapadera yoti ipeze njira zothana ndi ziwawa zokhudza ndale.

Mawu anu owonjezera?

Amayi 40 omwe alipo pano ngati aphungu a ku Nyumba ya Malamulo achita bwino ndipo apereka upangiri wofunikira pa chitukuko cha dziko lino. Nawo makhansala athu achitanso bwino ndipo ena adasankhidwa kukhala mafumu a mizinda ya m’dziko muno. Izi zimatipatsa mangolomera kuti zinthu zikuyenda, ndipo amayi akuchita bwino. Ife tikuona kuti nthawi yakwana yoti tipereke mwayi wokwanira woti amayi adzapikisane nawo pa zisankho za mu Sepitembala.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button