Anatchereza
Akuti tibwererane
Anatchereza,
Mmbuyomu ndidakwatiwa, koma banja lidatha ndipo ndidapeza mwamuna wina.
Banja ndi mwamuna wachiwiri uja lidathanso kaamba koti amakonda akazi kwambiri.
Mwamuna woyamba uja atamva zoti ndasiyana ndi mwamuna wachiwiri uja anabwera kwathu kudzandipempha kuti tibwererane.
Koma ndili pa chibwenzi ndi mwamuna wina yemwe akuthandiza mwana wanga opanda vuto lina lililonse pamene bambo wake sachitapo kanthu.
Gogo, nditani pamenepa?
PPJ
Mbayani,
Blantyre
PPJ,
Ndikupemphe kuti upeze mwamuna mmodzi wokhulupirika woti mumange naye banja ngati mukufuna kutero.
Paja amati nsabwe yoyendayenda imakumana ndi chala.
Ngati mukufuna kubwererani ndi mwamuna woyambayo, manja mfundo ndipo mutero koma musachite zoti ichi chakoma icho chakoma.
Koma mukakwatirana ndi mwamuna wachiwiriyo kodi bwenzi lanu lomwe likudzipereka kuthandiza mwana mwanu mutani naye?
Ndanena izi kaamba koti mukuoneka kuti wakopeka kale mtima ndi mwamuna woyambayo.
Ndalankhula izi chifukwa mukadakhala kuti mulibe naye chidwi simukadalemba kalata yofunsa nzeru poganizira kuti muli kale paubwenzi ndi mnyamata wina.
Mangani mfundo imodzi popeza pawiripawiri sipauzirika.
Natchereza
Musaopere kunjira
Anatchereza,
Ndine mtsikana wa zaka 30. Ukwati ndi mwamuna amene adandibere ana atatu udatha.
Mwachisomo cha Mulungu ndapeze mnyamata yemwe sanakwatirepo kapena kuberekapo ndipo akufuna tikwatirane.
Anatchereza, kodi ndilole kukwatirana naye?
Nanga makolo ndi abale ake akandilandira bwanji ine ndi ana anga?
Ndathedwa nzeru,
AWP
Salima
AWP
Nkhani yomwe mwatulutsa ndi yovuta chifukwa nthawi zambiri zimavuta kuti akuchimuna alandire mkazi woti ali ndi ana pamene wawo ndi mnyamata wosaberekapo.
Ngakhale timati banja ndi anthu awiri, koma makolo ndi abale ndi amakhudzidwanso kwambiri ndi banja la mwana wawo.
Ngati mwamukonda mnyamatayo, muuzeni nkhawa zomwe muli nazo kuti mumve maganizo ake.
Kambiranani mavuto omwe mukuwaona mtsogolo. Mukatero, fotokozerani abale anu za ganizo lanulo, komanso mnyamatayo akatule nkhaniyi kwa makolo ake.
Mukatero muona nokha ngati n’kotheka kupitirira ndi ukwatiwo kapena ayi.
Musachite kuopera kunjira chifukwa nthawi zina zomwe munthu umaganiza si zichitika amangokhala maganizo chabe basi. Mutha kudabwa akuchimuna atakulandirani ndi kuvomereza chomwe inu muli.
Natchereza
Ana owapeza avuta
Zikomo Anatchereza,
Ndakhala pachibwenzi ndi mkazi wina yemwe ndidalowa naye m’banja chaka chatha. Iye adabwera ndi ana ake awiri ndi abale ena ndipo polingalira kuti ndi banja, nanenso ndidakatenga mwana wanga.
Iye akungokhalira kulalatira mwana wangayo ati ndi wamwano. Nthawi zina akumachita izi panja kuti a nyumba zoyandikira amve. Akuti ngakhale nditachoka sangadandaule, chonsecho ali ndi pathupi pa miyezi 7.
Ndapirira mokwanira, ndithandizeni.
WL, Lilongwe.
WL,
Musanachite chilichonse pabanja
kukambirana kaye. Momwe zikuonekera apa, mkazi wanuyo adakangotenga ana ndi abale akewo musanakambirane. Nanunso mudangoyendera yanu nkukatenga mwana wanu.
Choncho kusamvana sikungalephere kubwerapo.
Komatu apa palibe chifukwa chokwanira choti nkuthetsera banja.
Khalani pansi nkumanga mfundo imodzi. Ndi ana ndi abale ati amene ayenera kuchoka pakhomopo ndipo ndi angati amene ayenera kuchoka?
Mukuyembekezera mwana wanu, kusonyeza kuti udindo wanu ukukula.
Ndikufuna banja
Gogo,
Ndine mnyamata wa zaka 23 ndipo ndikufuna mkazi womanga naye banja. 0888187696