Anatchereza
Agogo ndili ndi zibwenzi ziwiri koma onsewo ndi pachibale komanso amadziwana. Ndikawauza kuti andisiye onse amakana, nditani gogo chifukwa onse kwathu amabwera koma zundivuta kuthananazo?
Nkhani yanu ikutipatsa mafunso ambiri. Tikukhulupirira kuti amuna onsewo sadakufunsireni tsiku limodzi. Zikuonetseratu kuti aliyense adabwera payekha. Ndiye mutalola woyambayo, n’chifukwa chiyani mumalolanso wachiwiri yemwenso ndi mbale wa woyambayo? Izitu ndi zomwe mumafuna. Ngati mukufuna kuti akusiyeni, lekani kuwayendera, kuwayankha mafoni awo ndipo muchotse nambala zawo m’foni yanu. Musalole kuti afike pakhomo pano ndipo asiya.
Ndine VM ndimachokera ku Mulanje ndili ndi akazi atatu, ndidapezeka ndi akazi atatu chifukwa enawa amkandikonda kumayambiriro achikondi, kenako amayamba kupanga zofuna zawo. Ndiye panopa wina ali ndi mwana wa mng’ono, wina ndi woyembekezera komanso wina alibe mwana. Panopa onsewo ali payekhapayekha. Amawerengera kuti ali ndi mwamuna kunena ine, ndipo kwa ine onsewa ndimawaona chimodzimodzi, ndiye ine zikundivuta kusankha chonde thandizeni kodi ndisankhe uti? Onsewa akufanana zochitika zawo.
Bambo VM,
Penapake ndikuvutika kumvetsa chimene chidakupangitsani kuti mpaka mukhale ndi akazi atatu. Woyamba wakanika kupereka chikondi, wachiwirinso mpaka kukhala ndi wachitatu? Zovuta kumvetsa komabe muyenera kutenga amene ali ndi mwanayo. Ameneyo ndi woyamba enawo amupeza komanso kuli mwana amene akufunika chisamaliro chanu. Wachiwiriyo mudzitumiza thandizo kuti asamalire mimba ndipo mudzathandizebe mwana akadzabadwa. Wachitatuyo aone msana wanjira.
Ndine mnyamata wa zaka 29, ndidapanga chibwenzi ku Mangochi koma mkaziyo akukana kuti ndikaonekere kwawo.
Ndine C ku Thyolo.
Achimwene a C, chibwenzi nthawi zambiri chimakhala ndi ganizo limodzi kuti mawa mudzamange banja. Ameneyo banja sakulifuna chifukwa achikhala amalifuna bwezi atakhala woyamba kukuitana kuti ukaonekere. Uyu asakutaitseni nthawi, mulekeni azipita.
Chibwenzi changa chimandikaikira chifukwa amandigwira ndi ma message a zibwenzi zanga zakale. Nditani kuti adzindikhulupirira ine
T ku Zomba.
T,
Palibe munthu amene angakukhulupirire ngati ukuchezabe ndi zibwenzi zakale. Pamenepo palibe kukambirana. Ngati mukufuna wakale, bwereranikoni. Ngati mukufuna wapanoyo ndiye zonse zakale muzisiye ndiye akukhulupirirani.
Ndine DW ku Zomba, ndili ndi chibwenzi ndipo timakondana, koma pamene adachoka kupita ku holiday tidangolankhulana masiku ochepa, koma pano kuimba sakuyankha. Nditani?
DW,
Penapake timathamangira kuweruza pamene tilibe mfundo yogwirika. Kusayankha foni pena sizitanthauza kuti munthuyo wapeza wina. Dikirani adzabwerenso kapena adzayankhe foni ndipo mudzamve chimene chidamupangitsa kuti asamayankhe. Ngati sadzabweranso ndiye basi mutayeni.