Anatchezera

Akunyengana ndi mnzanga
Zikomo Anatchereza,
Ndakhala pabanja zaka 7 ndipo tilinso ndi mwana wa zaka 7. Tsiku lina mwanayo adathyoka mkono ndipo adatigoneka kuchipatala sabata ziwiri ndi masiku 4.
Ndili konko, ndidamva kuti mwamuna wanga akuyenda ndi mnzanga, yemwenso ndi woyandikana naye nyumba. Titatuluka adabwera kudzandiuza kuti mwamuna wanga adamufunsira koma adawakana.
Nditawafunsa amuna anga adakana. Chodabwitsa nchakuti, usiku mwamuna wanga amasowa. Kuyang’ana kuchimbudzi, kubafa ngakhalenso pakhonde osaoneka.
Ntawapanikiza, adaulula kuti amayendadi ndi mnzangayo. Powafunsa ngati ndili ndi vuto adati palibe, koma Satana ndiye adawanyenga. Ndichitenji?
EKM
EKM,
Amuna anuwo alibee chikondi chenicheni. Iwowo povomereza kuti amanyengana ndi mnzanu, aonetseratu ukamberembere wawo. Poyamba ndi kukana ndiye kusowa chikondiko.
Chokaikitsa china nchakuti mnzanuyo adabwera yekha kudzakuuzani kuti amuna anu adamufunsira koma adanama kuti adawakana. Ichi chidali chiphimba m’maso chabe chifukwa amadziwa kuti manong’onong’o a uhule wake akufikani.
Zikatere nkutani? Kunjaku kudaopsa ndipo si bwino kusekerera mwamuna kapena mkazi wosakhulupirika. Nthawi yoimbs nyimbo ya kapirire kunka iweko idatha.
Kaitureni nkhaniyi kwa ankhoswe chifukwa uwu ndi mlandu wachigololo choletsedwa ndi Ambuye.

Apachibale akundifuna
Anatchereza,
Pali anyamata awiri a pachibale amene akuoneka kuti amandifuna. Mmodzi mwa anyamatawo ndidamudziwa kalekale ndipo wakhala akundifunira koma ndimamukana.
Ndidadziwana ndi winayo chifukwa cha mbale wakeyo ndipo ndiye akunditumizira mauthenga a chikondi, ati akundifuna. Ndichitenji, chifukwatu awiriwo akundisowetsa mtendere.
M.E.
Mponela

ME,
Ngati anyamatawo simukuwafunadi ndi bwino kuwauziratu, mmalo mowapatsa banga kuti aziganiza kuti mwayi ukadalipo.
Mwinatu inuyo simutsindika kukana kwanuko. Komanso nkutheka kuti anyamatawo ndi nkhakamira. Mwinanso ali pampikisano kuti aone angakutengeni ndani.
Muli monsemo, mphamvu zili m’manja mwanu, kulola kapena kukana.

Ana owapeza avuta
Zikomo Anatchereza,
Ndakhala pachibwenzi ndi mkazi wina yemwe ndidalowa naye m’banja chaka chatha. Iye adabwera ndi ana ake awiri ndi abale ena ndipo polingalira kuti ndi banja, nanenso ndidakatenga mwana wanga.
Iye akungokhalira kulalatira mwana wangayo ati ndi wamwano. Nthawi zina akumachita izi panja kuti a nyumba zoyandikira amve. Akuti ngakhale nditachoka sangadandaule, chonsecho ali ndi pathupi pa miyezi 7.
Ndapirira mokwanira, ndithandizeni.
WL,
Lilongwe.

WL,
Musanachite chilichonse pabanja mumayenera kukambirana kaye. Momwe zikuonekera apa, mkazi wanuyo adakangotenga ana ndi abale akewo musanakambirane. Nanunso mudangoyendera yanu nkukatenga mwana wanu.
Choncho kusamvana sikungalephere kubwerapo.
Komatu apa palibe chifukwa chokwanira choti nkuthetsera banja.
Khalani pansi nkumanga mfundo imodzi. Ndi ana ndi abale ati amene ayenera kuchoka pakhomopo ndipo ndi angati amene ayenera kuchoka?
Mukuyembekezera mwana wanu, kusonyeza kuti udindo wanu ukukula. n

Share This Post

One Comment - Write a Comment

Comments are closed.