Anatchezera: Akukana kunditsata

Agogo,

Ndine mnyamata wa zaka 20 ndipo ndili pachibwenzi ndi mtsikana wa zaka 22 ndipo timakondana kwambiri koma vuto ndi loti akukana kunditsata kuchipembedzo changa. Ndiye ndithetse chibwenzichi kapena ndipitirize?

RM

 

Zikomo RM,

Choyamba ndikanakonda nditadziwa kuti cholinga cha chibwenzi chanu ndi chiyani, komabe poti ukufuna maganizo anga ndikuuza. Ndikhulupirira kuti cholinga cha chibwenzi chanu ndi kudzamanga banja mtsogolo, ngati sindikulakwa, ndipo ngati anthu muli ndi cholinga chodzakhala thupi limodzi ndi bwino kwambiri kuti muzigwirizana muzonse. Inde, pali mabanja ena oti mwamuma amapemphera mpingo wina ndipo mkazi nayenso amapita kwina, n’kumakhala bwinobwino mwansangala. Koma kunena zoona mukasiyana zipembedzo pamakhalabe kenakake kosonyeza kuti pali kusagwirizana m’banjamo. Ndiye ndi bwino kugwirizana chimodzi musanalowe m’banja. Munayamba mwakhala pansi n’kukambirana kuti chifukwa chake n’chiyani akukanira kukutsatira kuchipembedzo chako? Nanga iweyo sungamugonjere wachikondi wakoyo kuti umutsate kumpingo kwake? N’chifukwa chake nthawi zambiri kumakhala bwino inu achinyamata mukamafuna mnzanu wachikondi muzidyerera maso kwa anyamata kapena atsikana omwe mumapemphera nawo mumpingo umodzi. Nanga chokafunira wachikondi kwina n’chiyani? Ndiye wafunsa kuti kodi uthetse chibwenzichi kapena ayi? Ine ndikuti zili ndi iwe mwini mmene ukumvera mumtima mwako.

 

Ndipange bwanji?

Agogo,

Ndine mnyamata wa zaka 20 ndipo ndinakwatira mwangozi nditapereka mimba kwa mtsikana wina. Ndimafuna nditapitiriza sukulu koma zikukanika chifukwa mkaziyu akukana kuti nditero. Ndipange bwanji?

JK

 

Zikomo JK,

Ndakhala ndikulangiza anyamata ndi atsikana ambiri kuti mfulumiza adadya gaga, lero si izi waziona, mwana wanga? Ndakondwa kuti waona wekha kufunika kwa sukulu ndi kuipa koyamba kugonana ndi atsikana, komanso mosadziteteza, udakali pasukulu. Udakali msinkhu wopita kusukulu ndipo ndi bwino kwambiri utatero. Ngati mkazi wakoyo umamukonda ndipo iyenso amakukonda chimodzimodzi, ayenera kumvetsa cholinga chako choti upitirize maphunziro ako kuti kutsogolo mudzakhale moyo wabwino, wodzidalira nokha, osati mmene zilili panopa chifukwa mmene ndikuonera banja lanu lidalira makolo-chakudya, zovala, sopo amene ndi zina zotere. Umutsimikizire mkaziyo kuti kupitiriza sukulu sikutanthauza kuti banja lanu latha, koma kuti ukuganiza za tsogolo lanu ngati banja. Umuuze kuti sukulu simatha-akuluakulu amene mukuwaona m’maofesiwa ambiri afika pamene ali chifukwa chopitiriza sukulu ali m’banjabe. Tsono chovuta kuti iwe upitirize sukulu n’chiyani? Ngati iye safuna sukulu, zake izo, iwe chita zomwe ukufuna. Ndikhulupirira ngakhale makolo ako adzasangalala kwambiri kumva kuti ukufuna kupitiriza sukulu.

 

Ndinalapa

Anatchereza,

Ndinali m’chikondi kwambiri ndi mwamuna wa kwa Jali koma atandipatsa pathupi samandiuza nzeru iliyonse yothandiza pa umoyo wa mwana wodzabadwayo, mapeto ake anandipatsa ndalama zokachotsera pathupipo kuchipatala. Zotsatira zake ndinadwala kwambiri koma nditapeza bwino anayamba kundipepesa koma ine ndinamenyetsa nkhwanga pamwala kuti sindidzayambiranso. Kodi mwamuna wotsogolera zolakwa ndi wabwino? Koma ineyo ndinalapa, amama, ndipo ndinasiyana naye.

ML

 

Zikomo ML,

Ine ambiri ndilibe koma ndingoti khokhokho! Kumeneko ndiye timati kukula. Akulu akale adati mmphechepeche mwa njovu sadutsamo kawiri. Munthu ukachimwa ndi bwino kulapa monga wachitira iweyomu. Ndithudi mwamunayo sadakufunire zabwino ndipo chikondi chake chidali cha chiphamaso, basi; amangofuna zogonana koma osalabadira za zotsatira zake. Wachita bwino kumusiya ameneyo ndipo yamba moyo wina watsopano. Mwamuna wina akakufunsira mulole, koma osamulola kuti muyambe mwagonana musanalowe m’banja. Amuna ambiri akangowavulira musanalowe m’banja, sakhalanso ndi chidwi chifukwa amati “ngati wandilola, n’kutheka kuti adalolanso amuna ena”.

 

Share This Post