Chichewa

Apempha anthu kupanga manyowa

 

Sukulu ya aphunzitsi Development Aid from People to People (Dapp) Chilangoma ku Blantyre yapempha anthu kupanga manyowa kuti akhale ndi mbewu zathanzi komanso zochuluka.

Mkulu wa mapologalamu pasukuluyo, Hope Funsani, adanena izi Lachiwiri pamwambo wopereka chimbudzi chamakono m’dongosolo la School Garden and Nutrition (SGN) pa sukulu ya pulaimale ya Samama m’mudzi mwa Kamowa kwa T/A Kuntaja m’bomali.

Chimbudzicho, skyloo, chimalimbikitsa ukhondo ndi kupereka danga lopanga manyowa kuchoka ku ndowe za anthu.

Chimbuzi cha skyloo pa pulayimale sukulu ya Samama

Funsani adati manyowa amathandiza mbewu kupirira ku chiwawu chifukwa amasunga chinyotho kwa nthawi yaitali.

“Feteleza amaonongetsa ndalama, sabwezeretsa chajira m’nthaka ndipo timafunika kuthira chaka chilichonse. Manyowa amathandiza mbewu kukhala zathanzi, zochuluka ndipo umathira mmene wafunira. Banja lililonse likhalenso ndi polima ndiwo za masamba,” iye adatero.

Pothirira ndemanga pa chimbuzichi, mkuluyu adati chithandiza anthu kupanga manyowa ochuluka chifukwa azipeza ndowe zawo zomwe osati za ziweto zokha.

Mfumu Kamowa idayamikira Dapp kaamba ka chimbuzicho, koma idapempha thandizo ndi upangiri omangira zambiri kuti anthu apindule.

“Tadziwa kuti manyowa atithandiza kuthana ndi njala ikudza kaamba ka kusintha kwa nyengo. Ndilimbikitsa anthu kuchigwiritsa ntchito kuti tiyambe kusunga manyowa. Koma tithandizeni pomanga zambiri kuti banja lililonse lizisunga chinyontho chake,” adatero Kamowa.

Mphunzitsi wamkulu pasukulu ya Samama, Lameck Senzani, adati aonetsetsa kuti anthu akugwiritsa ntchito chimbuzicho moyenera kuti chiwapindulire.

Dapp imanga kaye zimbudzi za skyloo m’midzi 6 m’derali ndi thandizo la ndalama kuchoka ku Bonusan zomwe mikozo ndi nyasi zimapita magawo osiyana. Munthu akapambuka amayenera kuthira mbale ya dothi ndi ziwiri za phulusa zothandiza kuoletsa ndipo chimatsekedwa kwa miyezi itatu kuti manyowa apse. n

Related Articles

Back to top button