Chichewa
Atenge basi ndani?
Matimu a Nyasa Big Bullets ndi Mighty Be Forward Wanderers Lolemba akhala akukumana pampikisano wa Basi Ipite Soccer Fiesta wolimbirana minibasi ya K25 miliyoni pa Kamuzu Stadium mumzinda wa Blantyre.
Mkulu wa Luso TV Dick Juma Lachinayi adati basiyo, imene idafika m’dziko muno Lachinayi, ipitirira kusungidwa ndi bungwe la Football Association of Malawi (FAM) mpaka wopambana apezeke.
“Basi ndi imeneyi yafika lero ndipo mawa (Lachisanu) ikaperekedwa m’manja mwa FAM kuti ayisunge,” adatero Juma.
Iye adati adasankha matimuwa kaamba ka mavuto a mayendedwe omwe ali nawo ndipo akufuna kupereka mwayi woti opambana adziombole kumavutowa.
Masewero achibwereza alipo pa January 1 2017 ku Civo Stadium mumzinda wa Lilongwe. n