Nkhani

CDF idatsamwitsa aphungu, makhansala

Pomwe aphungu ndi makhansala amene agwira ntchito yawo kwa zaka 6 akwangula ntchito yawo Lachitatu, akadaulo ndi nzika zina anenetsa kuti mkokemkoke pa mbali ziwirizi ndi chimodzi mwa zopinga zimene zimachititsa kuti ntchito za chitukuko zisayende bwino.

Mwa malamulo, adindowa amayenera kukhala pa mipandoyi kwa zaka 5 koma kaamba ka kukanidwa kwa chisankho cha mtsogoleri wa dziko mu 2019 zomwe zidachititsa kuti Chisankho Chapadera chichitike mu 2020, bwalo lidagamula kuti aphungu ndi makhansala agwira ntchito kwa zaka 6 kuti adzamalizire limodzi ndi mtsogoleri wa dziko.

Aphungu adakwangula sabata yatha. I Nation

Polankhulapo pa momwe makhansala agwirira ntchito yawo, mkulu wa bungwe la Centre for Social Accountability and Transparency (Csat) a Willie Kambwandira ati ngakhale zambiri zayenda bwino m’zaka zimenezi, zotsamwitsa zina zinalipo.

“Panali kukokanakokana pakati pa aphungu ndi makhansala pa nkhani ya amene akuyenera kuyendetsa thumba la CDF. Aphungu ndi makhansala amagwira ntchito zawo mopikisana, mosadziwa ntchito yawo yeniyeni komanso mosakhulupirirana. Zimene zimadzetsa mpikisano wosafunika,” atero a Kambwandira.

Polongosola zina mwa zopinga zimene kayendetsedwe ka Nyumba ya Malamulo kanalili m’nyengoyi, kadaulo pa ndale a Ernest Thindwa adati kukhulana pa nkhani ya CDF kudasokoneza zinthu.

“Nzika sizimakhala ndi chonena pa nkhani za chitukuko. Nkhani ya CDF imalowetsedwa kwambiri ndale ndipo izi zimasonyezeratu kulephera kwa aphungu kuimira bwino nzika za m’madera awo,” adatero iwo.

A Thindwa adati monga zimakhalira m’nyengo ya aphungu, otsutsa boma amakokanakokana pa nkhani za ndale mmalo mokambirana zinthu zothandiza nzika za Malawi.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button