Chichewa

Chikondi chiphetsa amuna awiri

Listen to this article

 

Nthawi zina chikondi chikafikapo, chimazunguza mutu. Amuna awiri m’maboma a Machinga ndi Zomba adzikhweza sabata yathayi nkhani ya chikondi itavuta.

Mneneri wapolisi kuchigawo chakummawa Thomeck Nyaude watsimikizira Msangulutso za imfa ya Chrispine Botomani wa zaka 22 wa m’mudzi mwa Silulu kwa T/A Nkula m’boma la Zomba ndi Moses Ndege wa m’mudzi mwa Tchuka kwa T/A Chikwewu m’boma la Machinga.

Nyaude adati woyamba kudzipha adali Botomani amene adadzipha pa 25 October pamene adadzimangirira kunkhalango ya Chilunga mumzindawo.

Iye adati Botomani ankasalidwa ndi apongozi ake akazi pomunena kuti ndi mphawi ngakhale iye ndi mkazi wake akhala zaka zisanu ndi kudalitsidwa ndi mwana mmodzi.

 

“Mu 2013, mwamunayo adapita ku Lilongwe kukayang’ana maganyu. Apa makolo ake a mkaziyo adamuthawitsa mwana wawo kuti azikakhala ku Mangochi kwa achibale.

“Koma chifukwa chomukonda mwamuna wake, mkaziyo adadziwitsa Botomani za ulendowo ndipo mwamunayo adapita ku Mangochiko komwe adagwirizana kuti asinthe malo okhala,” adatero Nyaude.

Mneneri wa polisiyo wati awiriwa adasamukira kwa Chikanda m’boma la Zomba komwe amakhala pamene makolo ake a mtsikanayu amakhala ku Matawale m’bomali.

Koma wapadzala adavumbulutsa wa patsindwi pamene mkaziyo adauza mwamuna wake kuti amuperekeze kwa makolo ake koma ati adamuuzitsa mwamunayu kuti sakafika pakhomopo chifukwa amaonerana m’kodi ndi apongoziwo.

“Akumuperekeza, adakumana ndi apongoziwo. Adayamba kumutukwana motheratu zomwe zidakwihyitsa bamboyo,” adatero Nyaude.

Apa, iye adathamangira kunkhalangoko komwe adakadzikhweza koma ati adasiya kalata ya masamba anayi koma mbali imodzi ya kalatayo idati: “Apongozi mutsale bwino, mundisamalire mkazi wangayo padziko lapansi pano koma kumwamba tikakumana [ndipo] tikakwatirananso. Mundilelere mwana wanga….chikondi si chuma koma kugwirizana.”

Koma Nyaude wati palibe amene wamangidwa ndi imfa ya bamboyu ponena kuti palibe mlandu womwe wapalamulidwa.

“Mawu okha si mlandu. Inuyo kutukwanizana ndi mnzanu palibe mlandu ulionse. Ndiye palibe amene akuyenera kuzengedwa mlandu chifukwa cha imfa ya Botomani,” adatero Nyaude.

Pa nkhani ya ku Machinga, Nyaude adati malemu Ndege adakwatira akazi awiri omwe samasangalala kuti mwamunayo azipita kwa mkazi wina.

“Amayiwa amakhala nyumba zosiyana, ndiye mkazi aliyense adamupatsa masiku ake amene amakhala ndi bamboyo zomwe sizimasangalatsa akaziwa chifukwa aliyense amafuna mwamunayu akhale wake,” adatero.

Iye wati izi zidasokoneza bamboyu amene adaganiza zodzipha podzimangirira mkazi wake wamkulu ali kumunda pa 1 November 2015.

Related Articles

Back to top button
Translate »