Chichewa

Chulukitsani phindu la mtedza pobzala moyambirira

Listen to this article

Kuonjezera pa kuthawa ng’amba, woona za mbewu za mtundu wa nyemba ku nthambi ya kafukufuku wa zaulimi ya Bvumbwe m’boma la Thyolo Donald Siyeni akuti kubzala mtedza moyambirira kumachulukitsa phindu ku ulimiwu.

Iye adati izi zili chomwecho chifukwa kutalika kwa nyengo ya mvula ndi kofunikira kwambiri ku ulimiwu ndipo imachititsa zokolola za mbewuyi kuti zizisiyana ndi magawo 50 pa 100 aliwonse.

Mkuluyu adati kubzala mtedza moyambirira kumathandiza kuti ugwirizane ndi nyengo ya mvula mwachitsanzo mvula m’dziko muno imagwa m’masiku a pakati pa 120 ndi 140 amene akugwirizana ndi masiku amene mitundu ya mtedza ya chi Virginia imachera.

Alimi amene amabzala ndi mvula yoyamba amapindula ndi mbewuyi

“Mtedza oterewu umakhala ndi mwayi ogwiritsa ntchito mvula kwa nthawi yotalikirapo choncho umamera bwino ndi kukula mwamphamvu. Zotsatira zake umabereka ndi ndi khwima bwino chifukwa cha kupezeka kwa chinyonthochi m’nthawi yonseyi,” iye adatero.

Mkuluyu adati mlimi akabzala mtedza moyambirira umamera mosasiya mipata yochuluka.

Iye adati mbewuyi ikamera mosasiya mipata, imatetezeka ku matenda a chiwawu.

Siyeni adati izi zili chomwecho chifukwa chiwawu chimakonda pamalo pamene mtedza wamera mofooka ndi mwa patalipatali.

Kuonjezera apa, mkuluyo adafotokoza kuti mlimi akabzala mbewuyi mofulumira, imakula mwachangu choncho pamene matenda aziyamba kubwera, imakhala italimba.

“Mbewu zoterezi kumakhala kovuta kugonjetsedwa ndi matenda. Kubzala mbewuyi mwamsanga, kumathandiza kuti mtedza uike nthawi yabwino choncho umakhala ndi mpata wokwanira kuti mtedza weniweniwo uthe kukula ndi kukhwima bwino,” iye adatero.

Mkuluyu adaonjeza kuti kubzala mbewuyi nthawi yabwino kumathandiza kuchepetsa kugwidwa ndi chukwu pamene uli m’munda.

Iye adati izi zili chomwechi chifukwa siukumana ndi ng’amba imene imakolezera chuku ku mbewuyi ikakhala m’munda.

Mlangizi wa mbewu kudera la za ulimi la Lobi m’boma la Dedza Madalitso Machila adathirirapo ndemanga kuti kubzala mbewu ya mtedza moyambirira kumathandiza kuti imere bwino chifukwa dothi limakhala lidakali lotentherapo.

Iye adati izi zimachitika chifukwa mvula imakhala isadagwe kwa nthawi yotalikirapo.

“Mbewu monga mtedza, zimamera bwino nthaka ikakhala yotentherapo, isadazizire kwenikweni. Mlimi akadikirira kuti igwe kangapo, dothi limakhuta madzi zotsatira zake, imamera mosiya mpata,” iye adatero.

Iye adaonjeza kuti mlimi akabzala mbewuyi moyambirira, imakhala ndi mwayi wogwiritsa ntchito michere ya m’nthaka isadapite pansi kwambiri ndi mvula.

Mmodzi mwa alimi a mtedza m’boma la Dedza Mary Kantadza, adabwekera kuti atayamba kubzala mbewuyi ndi mvula yoyamba, zidamuchulukitsira zokolola zake.

“Ndisadaphunzire ulangizi woti tizibzala mbewuyi moyambirira ngati mmene timachitira ndi chimanga, pamunda waukulu ndi ekala imodzi ndi makololapo matumba a mtedza osaswa okwana 18 okha. Padakalipano ndi kumapeza matumba a mtedza osaswa okwana 42 pamalo omwewa,” iye adatero.

Mlimiyu adati ngakhale kuchite ng’amba, izi sizidamukhuza ulimi wake chifukwa pamene mvula imadukiza zake zimakhala zitayera kale.

Kantadza adavomereza kuti sabwereramo m’mundamu kubzala mbewu kachiwiri chifukwa umamera mosasiya mipata.

“Matenda amagwira ndithu mtedzawu koma ubwino wake zimakhala ukupita kokhwima kotero saphula kanthu,” iye adatero.

Mlimiyu adati chinsinsi chake kuti azibzala moyambirira chotere chagona pa kukonza m’munda ndi kupezeratu mbewu nthawi yabwino.

Related Articles

Back to top button
Translate »