Dodma ili chile pamene mvula yanunkhira

Listen to this article

Kunja kwacha pamene dziko lino likhale likulandira mvula posakhalitsapa malinga ndi kulosera kwa nthambi yoona za kusintha kwa nyengo ya Department of Climate Change and Meteorogical Services.

Kuloserako kwadzambatutsa nthambi yowona za ngozi zogwa mwadzidzidzi ya Department of Disaster Management Affairs (Dodma) yomwe yati posakhalitsapa iyamba kumwaza uthenga kuchenjeza Amalawi pa nkhani za ngozi zadzidzidzi.

Mneneri ku Dodma Chipiliro Khamula adati bungwe lake layamba kale zokonzekera pomanga midadada yoti anthu omwe adzakhudzidwe ndi ngozi za mtunduwo adzathe kukhalamo pogwiritsa ntchito ndalama zochokera ku bungwe la United Nations Development Programme (UNDP).

“Tikumanga midadada m’maboma omwe madzi amasefukira komanso tagula katundu yemwe tikumusunga kuti adzathandize anthu amene adzakhudzidwe,” adatero Khamula.

Mwezi wathawo mkulu wa Department of Climate Change and Meteorogical Services Jolamu Nkhokwe adauza dziko kuti chakachino kubwera mvula yabwino kaamba ka mphepo ya La Nina yomwe imaziziritsa Nyanja ya Pacific yomwe zotsatira zake ingadzetse mvula yochuluka ku mmwela kwa Africa kuphatikiza Malawi. n

Related Articles

Back to top button
Translate »