Jannah Theme License is not validated, Go to the theme options page to validate the license, You need a single license for each domain name.
Nkhani

Dolo ndi ndani mu chipeta ichi?

Pamene kwatsala masiku atatu okha kuti nzika za dziko lino zivote, atsogoleri omwe akuimira pa mipando ya upulezidenti, uphungu wa Nyumba ya Malamulo ndi ukhansala, mitima ili dakhidakhi.

Padakalipano, aliyense sakudziwa kuti mwamuna ndi ndani m’chipeta ichi.

A Mpesi: Amayi analembetsa ambiri

Bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) lidapereka masiku 60 oti atsogoleri atambasule mfundo zomwe zili m’manifesito awo.

Kampeni ikutha mawa ndipo atsogoleri 17 ndiwo akupikisana pa mpando wa upulezidenti.

Atsogoleriwa aponda pafupifupi boma lililonse mwa maboma 28 a m’dziko lino kufotokozera Amalawi mfundo zawo pa nkhani za umoyo, maphunziro, ulimi, ntchito, kutukula miyoyo ya amayi, achinyamata ndi anthu aulumali.

Nkhani yaikulu kwambiri pa kampeni ya chaka chino idali kukwera mitengo kwa zinthu zosiyanasiyana.

Pa zisankho za mmbuyomu Amalawi amavota mogwirizana ndi zigawo zawo.

Mwachitsanzo, anthu ambiri a m‘chigawo cha kummwera amavotera Democratic Progressive Party (DPP) pamene a m’chigawo chapakati adali pambuyo pa Malawi Congress Party (MCP).

Mkulu wa bungwe la National Initiative for Civic Education Trust, a Gray Kalindekafe, akuti ichi n’chifukwa chake atsogoleri omwe akuima pa mpando wa upulezidenti ndi achiwiri awo adakhazikika m’chigawo cha kumpoto.

“Chifukwa chigawo cha kumpoto sichitsatira chipani chilichonse, koma mfundo za mtsogoleri. Chigawo cha kumpoto ndi chimene chili ndi kuthekera kotulutsa boma latsopano,” iwo adatero.

Pa nyengo ya kampeni, zipani za DPP ndi MCP zakhala zikulozana zala kaamba ka ziwawa zomwe zachitika ku Kasungu ndi ku Machinga.

Mneneri wa MEC a Sangwani Mwafulirwa akuti anthu 7 200 905 ndiwo aponye mavoti Lachiwiri m’malo 6 331 omwe bungwe lidakhazikitsa m’maboma onse 28 a m’dziko muno.

Mwa anthu 7 200 905 omwe akuyenera kuvota chaka chino, amayi alipo 4 113 342 pamene abambo ndi 3 087 563.

Malingana ndi lipoti la bungwe la National Statistical Office, anthu okwana 10 957 490 ndiwo adayenera kuvota chaka chino.

“Mwa anthuwa, 5 146 679 adayenera kukhala abambo pamene 5 810 811 adayenera kukhala amayi,” adatero mkulu wa MEC a Andrew Mpesi.

Izi zikutanthauza kuti pa anthu 100 alionse oyenera kuvota, 66 ndiwo avote Lachiwiri likudzali.

Boma lomwe lili ndi anthu ambiri ovota, malingana ndi kaundula wa MEC, ndi Lilongwe (1 237 101) pamene Likoma ili ndi anthu ochepa (8 682) pa maboma onse 28.

Izi zikutanthauza kuti pa anthu 100 alionse omwe avote, 17 achokera m’boma la Lilongwe.

Maboma ena omwe ali ndi ovota ambiri ndi Blantyre (472 742), Mangochi (448 589),  M’mbelwa (371 399) ndi Kasungu (370 519).

Wapampando wa bungwe la MEC a Annabel Mtalimanja walengeza kuti ntchito yotumiza zikalata zovotera yayamba Lachiwiri ndipo itenga masiku atatu.

Iwo akuti makalata oyamba adapita ku Chitipa, Karonga, Likoma ndi Nkhata Bay.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button