Chichewa

Dzinja ladza, mphenzi zisautse

Listen to this article

Anthu akayambana m’madera ena mawu amakhala oti: Tikumana m’dzinja. Uku kumakhala kuopseza kuti akutumizira mphenzi.

Kodi n’kotheka kupha wina m’matsenga pomutumizira mphenzi? Nanga kodi izi zingatheke m’chilimwe?

Malingalirowa akudza pomwe mvula yayamba kugwa, ndipo a zanyengo achenjeza kuti mvulayi chaka chino idza ndi mphenzi, zimene zimadzetsanso mikangano ngati wina akanthidwa nayo.

M’chaka cha 2008, bungwe lofufuza za ziwerengero zina ndi zina la National Statistical Office (NSO) lidapeza kuti mwa Amalawi 100 alionse amene adacheza nawo, 78 ankakhulupirira ufiti, umene umabweretsa zinthu monga mphenzi zolenga.

Ngakhale ena mwa asing’anga amene tidacheza nawo adati n’zotheka kutumizira wina mphenzi, koma adasemphana pomwe ena amati izi zingathekenso m’chirimwe pomwe ena amati zimatheka m’dzinja basi.

Imodzi mwa nyumba zimene zidagumuka ku Balaka sabata yatha

Timothy Naluso, sing’anga wa m’boma la Phalombe, adati mphenzi imapangidwa kuchokera ku moto ndi mitengo itatu yotchedwa dzilodze ufe, nyesi komanso sitima ndi mankhwala a musupa pogwiritsa ntchito mvula.

“Timagwiritsa ntchito mvula pochita matsenga a mphenzi ndipo ngati munthu yemwe tikumufuna tamulephera ndiye kuti yemwe amafuna thandizoyo zimatha kumubwerera podwala nthenda ya chifufu,” adatero Naluso.

Koma kumbali yake Njoka Phiri wochokera m’boma la Ntcheu adati mvula imangokhala chongodzeramo chabe pofuna kudzibisa kaamba koti munthu wochita izi akhonza kuzindikiridwa mwachangu ngati sangagwiritse ntchito nyengo ya mvula koma matsenga a phenzi amatha kuchitika nthawi iliyonse.

“Timagwiritsa ntchito chipsolopsolo cha tambala chomwe timakachitchera kumanda ngati uta kenako timaphatikiza mitengo ina yomwe timanenerera pa chomwe tikufunacho zikatero chimafwamphuka kuchita zomwe tachituma,” adatero Phiri.

Naye Frank Gologolo wochokera m’boma ku Mulanje adagwirizana ndi Phiri ndipo adati nthawi iliyonse mphenzi za matsenga zimantha kugwiritsidwa ntchito.

“Chomwe chimachitika ndi choti timatuma ndondocha zome zimakhala kumanda kuti zitumize mphenzi kwa munthu yemwe tauzidwa ndiye ndondochazo zimapanga chifunga zikamakatula dziralo,” adatero Gologolo.

Mmodzi mwa akadaulo a zanyengo Elina Kululanga adati mphenzi imachitika ngati nyensi ya magetsi  ya magetsi pakati pa mitambo ndi nthaka.

“Ngoziyi imadza chifukwa mphamvu ya magetsiyo imakhala ikufuna kupeza njira yochoka kumwamba kupita m’nthaka ndiye ngati ipeza munthu kapena mtengo, kapena chilichonse chomwe ingathe kudutsa, makamaka zitsulo, imadutsiramo,” adatero Kululanga.

Koma malinga ndi mkulu wa nthambi yoona za nyengo Jolam Nkhokwe adati mphenzi ndi zachilengedwe ndipo chaka chino mvula ikhala ya mphenzi choncho anthu asamale.

“Pakufuna kuti Amalawi komanso magulu osiyanasiyana akhale ndi madongosolo a momwe angapewere ngozi zodza kaamba ka mvula monga mphenzi, kukokoloka kwa nyumba komanso mbewu,” adatero a Nkhokwe.

Iye adaonjezera kuti mvula yambiri igwa ku chigawo cha pakati ndi kummwera kwa Malawi.koma kuyambila mwezi wa January kufikira March dziko lonse lamalawi lizalandila mvula yochuluka.

Koma mneneri wa polisi m’dziko muno James Kadadzera wati Amalawi akuyenera kuonetsetsa kuti akutsatira malangizo omwe nthambi yoona zanyengo ikupereka.

“Nthawi ino anthu akuyenela kuonetsetsa kuti sakuoloka mitsinje yomwe madzi akuyenda chifukwa akhonza kukokoloka komanso apewe kuyenda pa mvula,” adatero Kadadzera.

Iye adatinso makolo awonetsetse kuti ana sakuyenda pa mvula.

Kumathero kwa sabata yatha, mvula yochuluka idaononga madera ena m’dziko muno.

Padakalipano, nthambi yoona za ngozi zogwa mwadzidzidzi yati mvula imene idatsakamuka sabata yatha yankhudza mabanja 613 ochokera m’maboma a Mzimba, Balaka, Mchinji ndi Mangochi.

Mneneri wanthambiyo Chipiliro Khamula n wati anthu awiri ochokera m’boma la Mchinji amwalira kaamba ka mphenzi yomwe idagwetsa chipupa cha nyumba.

“Kafukufuku akadali mkati kuti tidziwe kuchuluka kwa katundu yemwe waonongeka pa ngoziyi,” adatero a Khamula.

Iye adati mvula ya mphepoyi yakhudzanso maboma a Lilongwe komanso Salima ndipo nthambiyo yapereka katundu kwa mabanja omwe akhudzidwa m’maboma a Balaka ndi Mchinji ndipo pano akukonza zokapereka thandizoli ku Mzimba komanso Mangochi.

Related Articles

Back to top button
Translate »