Chichewa

GANIZO LOKWEZA FIZI LIBWERETSA NJIRIMBA

Listen to this article

 

Kudali matatalazi ku Nyumba ya Malamulo Lachinayi lapitali pamene aphungu adapindirana ndevu mkamwa pokambirana za ganizo la boma miyezi itatu yapitayo lokweza fizi m’sukulu zasekonadale ndi zaukachenjede m’dziko muno ndipo sizikudziwika kuti aphule poto ndani pankhaniyi.

Nkhaniyi idatentha m’Nyumba ya Malamuloyi pomwe aphungu, maka otsutsa ndi oima paokha, adadzudzula boma kuti silidakhoze pokwenza fizi m’sukuluzi kaamba koti panthawi ino Amalawi ambiri ali pamavuto aakulu a zachuma malinga ndi njala yomwe yagwa m’dziko muno.

Ngakhale mbali ya boma m’Nyumbayi idayesetsa kuti nkhaniyi isakambidwe, aphunguwo sadagonje mpakana mapeto ake adagwirizana kuti nkhaniyi ndi yofunika kuunikidwa modekha.

Adayambitsa nkhani: Jumbe
Adayambitsa nkhani: Jumbe

Boma, kudzera muunduna wa zamaphunziro, lidakweza ndalama zolipirira maphunziro m’sukulu za boma zasekondale ndi zaukachenjede ati pofuna kuchepetsa chipsinjo chomwe boma lidali nacho poyendetsa sukuluzi.

Panthawiyo, mneneri wa unduna wa zamaphunziro Manfred Ndovie adati kukwera kwa fiziku nkopindulira Amalawi chifukwa zithandiza kuti maphunziro apite patsogolo.

“Pali zambiri zomwe zikufunika kukonzedwa pankhani za maphunziro. Choyamba ndi malo ophunziriramo, zipangizo zophunzirira, malo ogona ndi chakudya. Kuti izi zisinthe mpofunika ndalama ndiye mukudziwa kale mmene boma lilili pankhani ya zachuma,” adatero Ndovie.

Koma phungu wa chigawo cha pakati m’boma la Salima, Felix Jumbe, yemwe ndi wachipani cha MCP, adati kukweza kwa fizi kwafika panthawi yomwe Amalawi ambiri ali ndi vuto la njala komanso mavuto a zachuma.

Iye adati zomwe boma lidaganizazi n’kufuna kusautsa anthu osalakwa omwe ali kale paumphawi wadzawoneni.

Aphungu ambiri adagwirizana ndi ganizo la Jumbe ndipo mmodzi mwa iwo ndi Esther Jolobala woima payekha, yemwe adati zomwe adanena Jumbe ndi ganizo lozama lofunika kuliona bwino.

“Ganizo lokweza sukulu fizi silidafike nthawi yabwino. Zimenezi zisokoneza makolo ambiri ndipo ine sindili muno kufuna kusangalatsa mbali ya boma kapena yotsutsa, koma anthu a kudera langa kummawa kwa boma la Machinga,” adatero Jolobala.

Nduna ya zachilungamo ndi malamulo Samuel Tembenu idayesetsa kuletsa zokambirana nkhaniyi ponena kuti nyumba ya malamulo ilibe mphamvu yosintha lamulo kudzera m’njira yomwe Jumbe adatsata.

Naye phungu wa kummwera kwa boma la Mangochi, Lilian Patel, wa chipani UDF, adati nkhaniyo si yofunika kukambidwa kaamba kakuti sidali pamndandanda wa nkhani zofunika kukambidwa, koma sizidamveke ndipo zidatengera sikikala wa Nyumbayo Richard Msowoya kulamula kuti nkhaniyo ikambidwe ndi kuunikidwa ndi aphunguwo.

Pambuyo pake aphungu adagwirizana kuti boma lisakweze fizi panopo mpaka mtsogolomu zinthu zikayambanso kuyenda bwino kumbali ya chuma.

Potsirapo ndemanga, mkulu wa mgwirizano wa mabungwe oona kuti maphunziro akuyenda bwino la Civil Society Education Coalition (CSEC), Benedicto Kondowe, adati kukweza fizi n’kofunika kuti maphunziro aziyenda bwino koma adati boma silidatsate ndondomeko yabwino.

Iye adati ndi mmene zinthu zilili panopa, anthu amafunika nthawi yokwanira kukonzekera osangoti lero ndi lero chifukwa Amalawi ambiri alibe ndalama.

“Kunena chilungamo m’Malawi muno muli mavuto. Omwe ali ndi ndalama ndi anthu ochepa kwambiri ndiye kukweza fizi panthawi yomwe anthu akukonzekera zaulimi si chanzeru. Akadayamba alengeza nkupereka nthawi yokonzekera,” adatero Kondowe.

Related Articles

Back to top button
Translate »